Tilibe mangawa ndi Gregory Gondwe, akuchocha kuzera Lilongwe timadziwa, akamabwera ndili okonzeka kukamulandira, atero a Kunkuyu

Nduna yofalitsa nkhani a Moses Kunkuyu ati ndiokonzeka kukachingamila mtolankhani Gregory Gondwe ku bwalo la ndege pofuna kusonyeza kuti boma lilibe mangawa ndipo kuti a Gondwe ndi mfulu kubwelela Ku Malawi.

A Kunkuyu ndi a Mkandawire pa msonkhano wa atolankhani ku Lilongwe

A Kunkuyu auza atolankhani Ku Lilongwe lero kuti pomwe a Gondwe amatuluka m’dziko muno kudzela Ku bwalo la ndege Ku Lilongwe, boma limadziwa komanso likudziwa anthu omwe anayenda ndi a Gondwe

Iwo ati izi zikutsimikizila kuti ngati boma likanakhala kuti linalidi ndi malingalilo ofuna kumanga a Gondwe akanathata kutelo.

Iwe ati a Gondwe akuyenela kubwelela Ku Malawi poti salipachiophsyezo china chilichonse.

Nduna ya zachitetezo a Harry Mkandawire yati boma lilibe mapulani aliwonse omanga mtolankhani Gregory Gondwe.

Malingana ndi a Mkandawire, boma lidauzidwa pamene a Gondwe amatuluka m’dziko muno kudzera pabwalo la ndege la KIA ndipo anafunsidwa ngati anali naye chifukwa chilichonse.

Malingana ndi a Mkandawire, boma lidavomera kuti aGondwe atuluke m’dziko muno chifukwa liribe nawo chifukwa.

 

 

Follow and Subscribe Nyasa TV :

Sharing is caring!

Follow us in Twitter
Read previous post:
Depressing! Ombudsman made 44 determinations last year, Govt only complied to 15

Office of the Ombudsman says that out of the 44 determinations released last year, only 15 were complied by the...

Close