A Polisi ku Nathenje amenya woyimba wokalamba Jetu kunsana, watero Dorothy Shonga

Apolisi ku Lilongwe anamenya kumsana kwa oyimba Jetu, watero mmayi wazamalonda Dorothy Shonga yemwe amadziwika kwambiri kuti Cash Madam.
Wamenyedwa: Jetu
Izi zinatsatira kusamvana komwe kunabuka pomwe apolisi ndi ena aku nthambi yotelera msonkho ya MRA paza zikalata za galimoto ya Dorothy yomwe anthuwa amayendera.
Malingana ndi Shonga yemwe wati chipwilikitichi chinadza kuyambila malo achipikisheni a Nathenje pomwe anthuwa amapita ku Blantyre.
Mukulemba kwake Shonga anati apolisiwa samakhutira ndi momwe iwo amafotokozera za umboni oti galimotoyo ndi yawo.
Apolisi anawauzanso kuti lamulo silitengera kuti munthu ndi otchuka kapena ayi.
Kutsatira kusamvanako, Shonga wati mmodzi mwa ofesala anamenya Jetu kumsana yemwe watchuka ndi nyimbo yotchedwa Chakwaza.
Shonga waonetsa malingaliro okamang’ala pa nkhaniyi ponena kuti akukhulupilira kuti apolisi akudzidwa kuti awaphwanyira ufulu komanso awachititsa manyazi pagulu komanso kuwanamizila kuti anali ndi galimoto yopanda zilolezo ndinso kuphonya mwayi otchita ntchito yamalonda.

Follow and Subscribe Nyasa TV :
Follow us in Twitter

4 replies on “A Polisi ku Nathenje amenya woyimba wokalamba Jetu kunsana, watero Dorothy Shonga”

  1. aPolice aku Malawi……. Kodi simuchita manyazi ndizochita zanu zofoilazi? Ndinu nomwe mwadulisa manja a mwana osalakwa uja, Lero mukumenya Gogo wachikulire Jetu. Is your training tel you that? You have to be serious when conducting your duties men in uniform please. Madam ZEZE, awoneseni a police osatha ntchito amenewa.

  2. Nde mmalo momenya Chongayo akukamenya munthu ot wangokwela nawo anthu enawa koma ngovuta kuwamvesa
    Pakufunika kufufuzapo pamenepo mwaukadaulo Jetu apepesedwe Iyo timat Arsenal pakwawo 😂

Comments are closed.