Tisalole kuti imfa zowawa takumana nazozi zisatigawanitse ngati dziko – Chakwera

Mtsogoleri wa dziko lino Dr. Lazarus McCarthy Chakwera wapempha aMalawi kuti asalolere kuti mdyerekezi agwiritse ntchito imfa zowawa zomwe dziko lino lakumana nazo pakatipa pobweretsa kugawanikana pakati pa anthu.

Chakwera wapemphanso mkulu wa apolisi mdziko muno kuti awonetsetese kuti nthambi ya polisi ikutumiradi anthu osati kuzunza anthu.

Iye wanene izi mu mzinda wa Lilongwe pamwambo wamapemphero womwe wakonzedwa pofuna kukumbikira kuti dziko lino lakwanitsa dzaka 60 lili pa ufulu wodzilamulira.

Chakwera anati akudziwa kuti pali kagulu kena kamene kakufuna kulowetsapo ndale pa ngozi ya ndege yomwe idapha a Chilima ndi anthu ena asanu ndi atatu (8).

Koma iye anatsindika kofunikira koti m’Malawi aliyense atengepo gawo potonthozana pamene dziko likupitirira kukhudza imfa zowawazi.

“Ntchito youzira mabalawa ndi yayikulu. Ndipo ntchito youzira mabalawa, njatonse. Ntchito youzirira mabalawa, nja inu atsogoleri azipembedzo chifukwa popanda mauthenga anu a chiyembekezo ndi mapemphero omulilira Mulungu, tikhoza kusokera ndi kuyamba kumunyozanso Mulungu yemweyo amene ali mtonthozi wathu,” anatero mtsogoleriyu.

Chakwera anapemphanso apolisi kuti asagwire ntchito yawo ndi mtima wofuna kuzunza omwe akulira malirowa mopyola muyezo.

“Chonde mokupemphani poti malamulo sakundilola kukulamulirani, ndimati ndikupempheni a Inspector General kuti muwonetsetse kuti Malawi Police Service ikutumikiradi ngati service osati ngati Malawi Police Force yopwetekera anthu,” anatsindika Chakwera.

Mtsogoleriyu anabwerezanso za kudzipereka kwake kutumikira ndi kukweza miyoyo ya aMalawi pogwira ntchito ndi aliyense mosatengera ndale kapena chilichose chomwe chimagawanitsa.

Chakwera anati pozindikira mabala omwe anthu ali nawo, achipatala komanso akatswiri akufukufuku pa ngozi ya ndege yomwe inachitika ndi omwe ali ndi mayankho owuzila mabalawa monga mwa ntchito iyo.

Asanayankhule mtsogoleriyu, m’busa Hamilton Yasin Gama, yemwe amatumikira ku mpingo wa CCAP ku sinodi ya Nkhoma, mu ulaliki wake, anachenjeza aMalawi kuti zovuta ndi zowawa zidakabwera.

Komabe Gama anatsindika kuti sikoyenera kulitembelera dziko ngakhale kunyozana koma kukhalabe anthu olungama.

Iwo anapereka chitsanzo cha Yobu yemwe chuma chake chonse chidatha, komanso ana ake onse kumwalira ndipo chilichonse chake chinachotsedwa tsiku limodzi, koma iye anakhalabe wangwiro padziko lapansi, ndi kuimabe njiii pamaso pa Mulungu.

“Dziko la Malawi limadziwika kuti ndilowopa mulungu, koma tivomeleze kuti machitidwe a anthu ambiri siowopa Mulungu,” anatero m’busayu.

Follow and Subscribe Nyasa TV :

Sharing is caring!

Follow us in Twitter
Read previous post:
Joggers on the move to support Matekenya Health Center

All is set for the 2024 Joggers On the Move (JOM), marathon competition which will be held on 3rd August,...

Close