Tonse yakanika kutumikira a Malawi, iyambe kupakila, chatero chipani cha DPP

Chipani chotsutsa boma cha DPP chati ulamuliro wa mgwirizano wa Tonse uyambe kuchotsera masiku ake okhala m’boma kaamba koti alephera kutumikira a Malawi.

Gavanala wachipanichi mchigawo chakumvuma Sheikh Imran Ntenje wati umoyo wa nzika ukupitilira kukhala wa umphawi mu zaka zinayi zomwe utsogoleriwu walamulira dziko lino.

Sheikh Ntenje wati katundu ofunikira monga chimanga, sugar komanso feteleza ndi zina, tsiku ndi tsiku zikukwera mtengo pa msika kusonyeza kulephera kwa boma lilipo panoli.

Iwo akuyankhula izi pamalo ochitira malonda a Lizulu m’boma la Ntcheu komwe akuluakulu achipanichi mchigawo chakumvumachi ali pa mdipiti omemeza anthu zolembetsa mu kaundula wa kalembera wa unzika.

Chisankho cha chaka chamawa cha 2025, bungwe la chisankho la MEC likuyembekezera kudzagwiritsa ntchito chiphanso cha unzika polemba anthu mukaundula wachisankhochi.

Follow and Subscribe Nyasa TV :

Sharing is caring!

Follow us in Twitter
Read previous post:
T/A Kawere hails NCA/DCA for promoting access to portable water in Mchinji

NCA/DCA joint country Program's TRANSFORM project has been hailed for improving access to portable water among communities in Mchinji district....

Close