UTM ipikisana nawo mchisankho cha chaka chamawa, watero Patricia Kaliati
A Kaliati ati UTM idakali ya mphamvu mzigawo zonse za mdziko lino ngakhale mtsogoleri wawo a Saulos Chilima adamwalira pa ngozi ya ndege.

Iwo ati akamaliza kukhuza maliro a Chilima ndi anthu ena asanu ndi atatu chipanichi chichititsa misokhano mzigawo zonse kuwuza Amalawi za tsogolo la chipanichi.
“Mchipani chathu mukulowa anthu a zipani zosiyanasiyana kufuna kukwanilitsa masomphenya omwe malemu Chilima anali nawo,” atero a Kaliati.
Ndipo mkulu wa a chinyamata mchipanichi Penjani Kalua, yemwe amadziwika ndi dzina loti Fredokiss, wapempha achinyamata kuti akalembetse ziphaso za umzika kuti adzakhale ndi mwai woponya voti.