Ras Chikomeni akugulisa chamba kusaka ndalama yopereka ku MEC kuti azayime pa chisankho 2025

Yemwe akufuna kudzayimira nawo pampando wa pulezidenti pa chisankho cha 2025 a Ras Chikomeni Chirwa wati wayamba kugulitsa chamba kuti apeze ndalama zomwe zimafunikira kupereka ku bungwe la MEC kuti munthu ayimire nawo pa chisankho .

A Chirwa akuti mpingo wawo wama Ras unalandira chiphaso chowavomereza kugulitsa chamba kwa chaka chimodzi kuchokera kubungwe lowona za ulimiwu la CRA ndipo ayamba kugulitsa chambachi kuti apeze ndalama zokwanira.

 

Malinga ndi a Chirwa,akugulitsanso ma T-shirt kuti apeze ndalama zokwanira zogwiritsa ntchito kukonzekera chisankho cha 2025 ndipo wapemphanso aMalawi kuti amuthandize.

 

Katswiri pa nkhani za ndale a Chimwemwe Tsitsi wayamikira a Ras Chikomeni kaamba koyamba pawokha kusaka ndalama ndipo awalangizanso kuti afikira anthu omwe ali ndikuthekera kowathandiza.

 

Follow and Subscribe Nyasa TV :

Sharing is caring!

Follow us in Twitter
Read previous post:
Blantyre health centres provided with motorcycles for direct delivery of routine immunization vaccines 

Blantyre District Health Office (DHO) has provided 18 motorcycles to health centres under its jurisdiction for direct delivery of routine...

Close