Vitumbiko Mumba wapita basi! BT CCAP yati ndiyokondwa ndi iyeyu chifukwa utsogoleri ulimo mwanyamatayi

Mmodzi wa anthu amene akufuna kupikisana nawo pa udindo wa wachiwiri kwa mtsogoleri wa chipani cha MCP a Vitumbiko Mumba walonjeza kuthandiza Blantyre CCAP Synod m’magawo osiyanasiyana.

Vitumbiko Mumba

A Mumba ayankhula izi pa mpingo wa Mount Carmel CCAP mu mzinda wa Blantyre pamene adali nawo pa mwambo wolandira a Anderson Juma kukhala m’busa wa mpingowu.

Mwazina, a Mumba apereka ndalama yokwana K5 miliyoni kuti zithandizire pa ntchito zosiyanasiyana pa mpingowu.

 

Iwo aperekanso K1 miliyoni kwa a Juma komanso ati adzithandiza amayi a chigwirizano pa mpingo wa Mangochi CCAP.

A Juma, kupatula kuthokoza pa mphatsozi, adati ndi wokondwa kudzatumikira pa mpingowu ndipo alonjeza kugwira ntchito limodzi pokuza moyo wa uzimu wa akhristuwa.

 

Follow and Subscribe Nyasa TV :
Follow us in Twitter