Woyimba wazaka 74, Jetu, alandira plot kuchokera ku Eagles Real Estate Consultants

Kampani yogulitsa malo ya Eagles Real Estate Consultants yapeleka plot kwa oyimba Jetu yemwe dzina lake lenileni ndi Christina Kholiyo pomulimbikitsa pa ntchito yake yoyimba komanso kusangalatsa anthu.

Jetu kulandila plot yake

Mkulu owona za malonda ku kampaniyi a Roshan Thole wati plot-yi yomwe ili ku Lilongwe ku Airwing ndi ya ndalama zosachepra K6 Million Kwacha ndipo iyi ndi mbali imodzi yothandiza mzimayiyu kuti akhale ndi nyumba yake.

Poyankhula atalandira malowa a Jetu a zaka 74 omwe abeba ndi nyimbo ya Chakwaza panopa anati sakukhulupilira kuti izi zachitika kamba koti anali maloto chabe pachiyambi.

Ndondomeko yothandiza mzimayi oyimbayu inatumphuka ndi aja amadziwika kuti Dorothy Kingston atawona kufunika kotero ndipo apempha anthu akufuna kwabwino kuti apitilize kuthandizapo kuti amangire nyumba Jetu.

 

Follow and Subscribe Nyasa TV :

Sharing is caring!

Follow us in Twitter
Read previous post:
Gender activists angry at DPP for appointing Chaponda not Navicha for the position of the Leader of Opposition

Gender activists have expressed disappointment with the U-turn by the Democratic Progressive Party (DPP) on the appointment George Chaponda as...

Close