Zachitika! A polisi ndi akhonsolo ya Lilongwe agumula masitolo omangidwa mmanda ku Area 25
Ku m’banda kucha lero loweluka achitetezo komanso akhonsolo ya mzinda wa Lilongwe, agumula komanso kufwafwaniza masitolo omwe anthu adamanga m’manda ku Nsungwi ku Area 25.
Malingana ndi anthu omwe anaona izi zikuchitika, ati achitetezowa anafika chama 1 koloko m’banda kucha, ndipo anatseka nseu wa Nsungwi kuyamba kugwira ntchito yawo.
Ena mwa omwe tayankhulana nawo pamalowa atiuza kuti, anthu ena anatengelapo mwayi kuba katundu yemwe eni sitolo onyalanyaza sanasamutse atalandila chenjezo.
Ku m’mawaku tapeza anthu ochuluka akutola zotsalira mwa zomwe zaonongeka.