Zachitika: Paul Banda walandira K14.5m yomwe a Malawi asonkha kuti ithandize malipiro akuchipatala
Oyibma Paul Banda lero walandira ndalama zokwana K14.5 miliyoni zomwe a Malawi, motsogozedwa ndi Onjezani Kenani, asonkha kuti zimuthandize kulandira chithandizo kuchipatala. Katswiri oyimbayu akudwala matenda a ipso ndipo wapatsidwa ndalama zi ku nyumba kwake kwa Chatha ku Chileka mu mzinda wa Blantyre.Mukuyankhula kwawo akuti kuthokoza kwake kukuwavuta chifukwa samayembekezera zoterezi.
“Zikanakhala a Malawi timathandizana chonchi, bwenzi zambiri zikuyenda,” anatelo Banda.M’modzi mwa anthu amene watenganawo gawo pa ntchito yi, McWilliams Mhone wati ndi othokoza kwa a Malawi onse amene atenga mbali posonkha ndalama zi.
Anatelo a Mhone: “Paul Banda ndi kholo la oyimba mu dziko muno.
Wagwira ntchito ndi oyimba ambiri ndipo vuto lake ndi vuto la dziko lonse.”
M’modzi mwa oyimba m’dziko muno Wycliffe Chimwendo wati ndi chikhulupiro chake kuti a boma aloweraponso kuthandiza Paul Banda malinga kuti zofuna zawo ndi zochuluka.
Follow and Subscribe Nyasa TV :