A Chakwera amazitamandira ndi ntchito zomwe zinayambika nthawi ya DPP, atero a Navicha

Mtsogoleri wa chipani cha DPP ku Nyumba ya Malamulo, Mary Navicha, wadzudzula boma la Tonse kamba kodzitamandira pa ntchito zachitukuko zomwe zidayambika panthawi yomwe DPP inali m’boma.

Izi zadza pomwe nduna zosiyanasiyana za mbali ya boma zimafotokoza zina mwa ntchito zachitukuko zomwe zikuchitika mdziko muno m’maboma osiyanasiyana.

Polankhula , Mary Navicha yemwe adasankhidwa kukhala mtsogoleri wachipani cha DPP posachedwapa, wadandaula kuti boma lalephera kumalizitsa ntchito zachitukuko munthawi yabwino ngakhale ndalama zomalizitsitsira zitukuko zi zidali zitaperekedwa kale  DPP ili m’boma .

Kuonjezera apo, Navicha wati pakufunika kuti boma la tonse liyambe kuyamikila ntchito ndi maziko abwino omwe  DPP idakhazikitsa mmbuyomu.

Mary Navicha

Follow and Subscribe Nyasa TV :

Sharing is caring!

Follow us in Twitter
Read previous post:
Zomba to have state-of-art stadium, government announces

Local Government minister Richard Chimwendo-Banda has told Parliament this morning that plans are in the pipeline to construct state of...

Close