A polisi awiri amangidwa ku Karonga pothandizira kulowesa mowa mu cell

Apolisi amanga a polisi anzawo awiri, omwe amagwira ntchito ku polisi ya Karonga, powaganizira kuti akukhudzidwa ndi nkhani yolowetsa mowa komanso lamya za mmanja mu chitokosi cha apolisi m’bomali.

Kalaya has confirmed the arrest

Kumangidwa kwa apolisiwa kukudza pomwe kanema ina inafala pa masamba a mchezo imene imaonetsa anthu omwe akuwaganizira milandu yosiyanasiyana akumwa mowa koma ali m’chitokosi.

Malingana ndi mneneri wa polisi m’dziko muno a Peter Kalaya, apolisi amangidwawa ndi Sub Inspector Kaston Matemba ndi Constable Brighton Mpombeza omwe akayankhe mlandu wa kulephera kusunga mwambo wa apolisi (Conduct at Police) komanso kusagwiritsa bwino ntchito udindo wawo (Abuse of Office).

Oganiziridwa apita nawo kubwalo la milandu posachedwapa.

Follow and Subscribe Nyasa TV :

Sharing is caring!

Follow us in Twitter
Read previous post:
Medical waste management to improve at Kasungu Hospital as incinerator is installed

Kasungu District Hospital has installed a new modern incinerator to destroy medical waste at the hospital. Similar project is taking...

Close