Akhristu a Mpachika CCAP adzudzula m’busa Ntepiha kuti akugwiritsa ntchito zithumwa pofuna kuthana ndi atsogoleri

Akhristu a mpingo wa Mpachika CCAP m’mzinda wa Blantyre adzudzula m’busa wawo, a Raphael Ntepiha, kuti akugwiritsa ntchito zithumwa pofuna kuthana ndi atsogoleri ampingo omwe akutsutsana ndi maganizo awo.

M’busa Ntepiha

Amene watipatsa nkhaniyi akuti nkhondo ya pakati pa akhristu ndi abusawa inafika pachimake Lolemba lathali pomwe abusa a Ntepiha adakawaza mankhwala kuzungulira tchalitchi uku akutchula maina a atsogoleri omwe iwo akufuna kuthana nawo.

Nkhaniyi inayamba mmbuyomu chaka chatha pomwe mkulu wina wampingo analemba kalata kuti ma executive members ampingo wa Mpachika CCAP akunyoza abusa. Ndiye abusa anangokwiya ndikuchotsa executive yonse asanafufuze nkhaniyo. Izi zinayamba kuwayipira akhristu ndipo anapempha executive kuti akapemphe ku likulu laling’ono,presbytery, kuti abusawa achotsedwe pakuti anali atangokhala miyezi yochepa pa Mpachika CCAP,” adatero yemwe adatitsina khutu.

Mkuluyo adatipatsanso chithunzi chomwe chikuwonetsa abusawo akuwaza mankhwala kachisi wa Mulungu’yo.

Nde zomwe zikuchitika pa chithunzipa ndi zakuti abusawa amawaza madzi kumatsirika church ndi cholinga chakuti anthu amwe anamata ma poster osonyeza kukwiya ndi khalidwe la abusawa awone zoopsa mpaka akapepese. Madzi osilikilawo anawatenga mu basin yomwe munali madzi obatizira ana pa 31/12/2023 ndipo akuti analengeza kuti madziwo asatayidwe pakuti akufuna kuthana ndi onse osawafunira zabwino. Moti pano makolo omwe ana awo abatizidwa akuderankhawa kuti mwina anawo ayikidwa mizimu yoyipa (dziwanda),” iwo adatero.

Abusa a Ntepiha sadatiyankhe titawafunsa za nkhaniyi. Koma akhristu a pa mpingowu atsindika kuti sakhala chete mpakana m’busayu atachoka.

Iwo akuti ndi okonzeka kukachita m’bindikiro pofuna kukakamiza m’busayu kuti apite malo ena.

Follow and Subscribe Nyasa TV :

Sharing is caring!

Follow us in Twitter
3 Comments
newest
oldest most voted
Inline Feedbacks
View all comments
Amzer
Amzer
4 months ago

Nkhani yabwino bwino ija mwaiyitathauziliraso mwina….

Lackson phiri juma
Lackson phiri juma
4 months ago

Paliso kuwa khulupilira awa?😒

Mwaxy
Mwaxy
4 months ago

Nkhani mwalemba apayi njaboza. The issue is that executive ya Mpachita CCAP yonse idachotsedwa mma udindo awo akuruakuru a mpingo wa CCAP atazindikira kuti panali kuti panali zolakwika Zina zomwe adindowa amachita. Ndi mbusayu yemwe anavumbulutsa zolakwikazi.

Tsono powawidwa kuti achotsedwa mmaudindo mpomwe ayamba propaganda yopita ku ma media house ndi nkhani za boza ngati izi. Koyamba kunali ku MBC pa nkhani za mmaboma komwe amatinso kuluyu amalezera Mpaka tapsa mzomwe mzaboza ndithu.

Read previous post:
Mpachika CCAP Christians, church minister lock horns over ‘juju’ use to attack Parish Committee members

A fierce warfare has erupted between Christians at Blantyre-based Mpachika CCAP Congregation and their resident minister, Reverend Raphael Ntepiha, over...

Close