Amila ndi kumwalira akufuna kuba nsomba mumisampha ya eni ku Mangochi

Zachitika ku Mangochi pamene bambo wa zaka 30 wamwalira atamila panthawi yomwe amafuna kuba Msomba mu misampha ya asodzi anzake.

Mneneli wapolisi ya Mangochi Amina Tepani Daudi watsimikiza za nkhaniyi ponena kuti mkuluyu ndi Issah Kamwendo ochokera m’mudzi mwa Namasiyano mfumu yaikulu Chimwala m’boma la Mangochi lomweli.

Malipoti ati pa 26 February 2024, mkuluyu adazemba pakati la usiku mkupita pa doko lina m’nyanja ya Malombe komwe anayamba kuwonjola Msomba m’matchela anzake.

Koma ali mkati mwakuba, eni matchelawa anatulukira zomwe zinapangitsa kuti mkuluyu adumphire m’madzi mkuyamba kuthawa.

Koma atadumphira m’madzimu, mkuluyu sanaonekenso zomwe zinapangitsa kuti anthu ayambe kufufuza.

Madzulo apa 27 February 2024, thupi la mkuluyu linapezeka likuyandama pa doko lina.

Kafukufuki waza chipatala waonetsa kuti a Kamwendo amwalira kaamba kobanika.

 

Follow and Subscribe Nyasa TV :

Sharing is caring!

Follow us in Twitter
Read previous post:
PS Gomani Chindevu says govt committed to good governance, transparency

Principal Secretary (PS) for the Ministry of Local Government, National Unity and Culture, Dr. Elizabeth Gomani Chindebvu, says the government remains...

Close