Boma la German lapereka ndalama zokwana K35 billion kudziko la Malawi za mtukula pakhomo

Boma la Dziko la German lero lapereka ndama zokwana K35 billion zomwe zigwire ntchito ya mtukula pakhomo.

Mukulankhula kwawo, nduna yazachuma a Simplex Chithyola Banda adayamika boma la Germany kamba ka thandizo la chuma chochuluka onga ichi.

A Chithyola alonjeza dziko la German kuti ligwiritsa ncthito bwino chuma chomwe boma la German lapereka ku boma la Malawi. A Chithyola alengezaso kuti ndalama za mtukula pakhola zikweranso pompano kamba ka ndalama zimenezi.

Iwo adati boma lionjezeraso chiwerengero cha a Malawi omwe amapindula ndi ntchito za mtukula pakhomo. Mmawu awo, nduna yowona kusasiyana pakati pa amai ndi abambo , a Jean Muona owauza Sendeza nawo athokoza boma la German kamba ka chuma chimenechi.

A Sendeza adati pompanoso boma la German laperekaso Magalimoto anayi oti athandizire ntchito ku undunawu. A Sendeza ati ndalama zimenezi zithandiza kwambiri kusintha miyoyo ya anthu ovutika maka a kumudzi.

Follow and Subscribe Nyasa TV :

Sharing is caring!

Follow us in Twitter
Read previous post:
NICE volunteers complain of ‘poor public service delivery’: Things are going astray

As the general public continues to complain about poor public services delivery through various governmental departments and agencies, NICE Trust...

Close