Boma layamba kumva maganizo a anthu pa ndondomeko ya maphunziro

Pamene ntchito younikanso ndondomeko ya maphunziro ili mkati, unduna wa za Maphunziro wati wayamba kumva maganizo a anthu pa zimene angafune kuti ziganiziridwe mu ndondomeko ya maphunziro ya tsopano.


Undunawu ukuchita kauniuniyu mogwirizana ndi bungwe laboma la Malawi Institute of Education (MIE).

Malingana ndi kalata yomwe undunawu walemba, kauniuni ameneyu ndiwokhudza maphunziro a m’sukulu za mmerampoyamba, za pulayimale, sekondale komanso koleji ya aphunzitsi a pulayimale.

Undunawu wati cholinga cha kauniuni wa ndondomeko ya maphunziroyi ndi kuwonesetsa kuti maphunziro  akugwirizana ndi zokhumba za Amalawi monga momwe masomphenya a dziko lino a Malawi 2063 amafotokozera.

“Ndondomeko ya maphunziro imathandizira kusula nzika kuti zikhale zaukadaulo zomwe zingathandizire kukweza chuma chadziko lino powapatsa nzeru, maluso ndi upangiri omwe ungawathandize kukhala odalirika paliponse. Imodzi mwa njira MIE lichite ndi kuchititsa misonkhano yomva maganizo a anthu pa zomwe angafune kuti ziikidwe mu ndondomeko ya maphunziroyi,” yatero kalata yomwe yasayinidwa ndi Dr. Rachel Chimbwete Phiri.

Kalatiyi ikupitiriza kunena kuti Unduna wa za Maphunziro umazindikira ndikuyamikira nzeru ndi maluso omwe nzika zili nazo zomwe zingathandizire kukweza maphunziro m’dziko muno popereka maganizo awo.

Motero, undunawu ukuyitana makolo, makomiti apa sukulu, ochita malonda, mafumu, atsogoleri a zipembedzo, mabungwe omwe siaboma, achinyamata, alimi, oimira mabungwe osiyanasiyana a m’madera ndi ena onse kuti akakhale nawo pa misonkhanoyi yomwe ndiyofunikira kwambiri.

Misonkhanoyi ikhala ikuchitika m’madera 18 a zigawo zonse zisanu ndi chimodzi (6) za maphunziro m’dziko muno. Misonkhano yofunsa maganizo a anthuyi ichitikira ku Maghemo Secondary School Hall pa 16/01/2024, nthawi ya 8:30 mmawa,    Mzimba Secondary School Hall pa 18/01/2024, Katoto Secondary School Hall pa 20/01/2024, Chayamba Secondary School Hall pa 16/01/2024      kuyambira 8:30 mmawa, pa        Dowa Secondary School Hall msonkhanowu udzachitika pa    18/01/2024 ndipo pa Nsalura Secondary School Hall        msonkanowu udzachitika pa 20/01/2024.

Misonkhano ina ikachitikira ku Ntcheu Secondary School Hall pa 16/01/2024, Mchinji Secondary School Hall pa 18/01/2024, pa Chinsapo Secondary School Hall        20/01/2024        , Mangochi Secondary School Hall pa 16/01/2024, Balaka Secondary School Hall pa 18/01/2024 ndi Mulunguzi Secondary School Hall      pa 20/01/2024.

Ina ikachitikira ku Chikwawa Secondary School Hall pa 16/01/2024, Mwanza Secondary School Hall pa 18/01/2024, Chichiri Secondary School Hall pa 20/01/2024        , ku Mulanje Secondary School Hall pa 16/01/2024, Luchenza Secondary School Hall pa 18/01/2024 ndi Phalombe Secondary School Hall pa 20/01/2024.

“Kupezeka kwanu komanso kutenga nawo mbali pa misonkhanoyi kuthandizira kusintha kwa maphunziro komwe zotsatira zake ndi kukhala ndi nzika za ukadaulo wabwino zomwe zingathandize kutukula chuma cha dziko lathu. Kuti dziko likhale lotukuka pa chuma ndi kofunika kuti mutenge nawo mbali posintha maphunziro.  Mukatero, maphunziro athu adzakhala okomera wina aliyense komanso osakondera zomwe zidzachititse kuti dziko lathu lithe kukwanilitsa masomphenya ake,” atero a Chimbwete Phiri.

A Chimbwete Phiri alangizanso Amalawi omwe sangapite ku misonkhanoyi kuti atomize maganizo awo polemba kalata ndi kutumiza ku:

The Executive Director

Malawi Institute of Education

P.O Box 50

DOMASI.

Amalawi atha kuperekanso maganizo awo kudzera mu njira zamakono monga WhatsApp pa namala iyi: 0990088035, komanso ku uthenga wotumiza kudzera pa makina a intanet pa: [email protected].

“Mukafuna kudziwa zambiri, imbani thenifolo kwa Ofalitsa nkhani ku MIE a Moses Mailosi pa 0881 737 157/0998544461,” atero a Chimbwete Phiri.

Follow and Subscribe Nyasa TV :

Sharing is caring!

Follow us in Twitter
Read previous post:
Malawi Bishops Vs Vatican: Did local Bishops disrespect Pope Francis over gays’ position?

Episcopal Conference of Malawi’s (ECM) stands to disrespect head of Catholic Church Pope Francis’ controversial decision to allow priests to...

Close