Bwanjinso? Aford yayimitsa msonkhano wake waukulu

Chipani cha Alliance for Democracy (AFORD) chayimitsa msonkhano wake waukulu omwe umayenera kuchitika mu mwezi wa Epulo mpaka sabata yoyamba ya Julayi chaka chino, ponena kuti akadakachitabe zina zokonzekera.

Polankhula, mtsogoleri wa chipanichi a Enock Chihana wati mwa zina, pali akulu akulu ena omwe akhale akulowa mchipanichi posachedwapa, ndipo akufuna kupereka mpata kwa anthu otere kuti apikisane nawo pa msonkhano waukulu.

Padakali pano, katswiri pa ndale a Ernest Thindwa wati nthawi zambiri zipani zambiri m’dziko muno zimasowa ukadaulo komanso dongosolo poyendetsa misonkhano yotere.

Chipani cha AFORD chidakatha kukhala choyamba kuchititsa msonkhano wawo mwezi wa Epulo chaka chino pamene tikuyandikira ku chisankho cha 2025.

Chipani cha MCP chidalengeza kuti chichititsa msonkhano wake mu mwezi wa August ndipo chipani cha DPP mu July chaka chino.

 

Follow and Subscribe Nyasa TV :

Sharing is caring!

Follow us in Twitter
Read previous post:
Rotary international president visits Malawi for collaboration is life serving development projects

Rotary family in Malawi has announced the coming of Rotary international president Gordon Maclnally to Lilongwe on March, 26th until...

Close