Chakwera Akwanitsa Lonjezo Lobweretsa Ogula Fodya Ambiri
M’mawu ake otsegulira msika wa fodya wa chaka cha 2025 ku Kasungu, Purezidenti wa Malawi Dr. Lazarus McCarthy Chakwera watsimikiza kuti wabweretsa ogula fodya ambiri monga momwe analonjezera. Izi zachitika pa tsiku lofunika kwambiri pa chuma cha dziko, ndipo Purezidentiyo anapereka mawu amphamvu otsindika kufunikira kwa mlimi wa fodya komanso thandizo la boma lake pa ntchitoyi.

Chakwera ananena kuti mlimi wa fodya ndi munthu ofunika kwambiri pa chuma cha Malawi chifukwa cha forex yomwe amalowetsa m’dziko. Iye anatsindika kuti ndalama zomwe mlimi wa fodya amalowetsa ndizo zomwe zimathandiza boma kugula mafuta, mankhwala, fetereza komanso zolipira odwala omwe amapita kuchipatala kunja. “Palibe munthu mdziko muno amene moyo wake siukhuzidwa ndi mlimi wa fodya,” adatero Chakwera.
Iye adanenanso kuti ngakhale dziko lakhala likukumana ndi mavuto monga ng’amba yomwe yawononga chimanga komanso kukwera kwa zinthu, zimenezi zikuyesedwa kuthandizidwa ndi ndalama zomwe dziko likulandira chifukwa cha fodya. Chifukwa cha udindo umenewu, Chakwera adati sasiya kuthandiza alimi a fodya mpaka chaka cha 2030, akamaliza nthawi yake yatsogolo monga Pulezidenti.
Purezidentiyo anatsutsa atsutsa omwe, malinga ndi iye, akungokonda mademo osathandiza dziko, pomwe iwo sakulimbikitsa ulimi wa fodya umene ukubweretsa chuma chenicheni. “Katsutsidwe ka boma koteroko ndi katsutsidwe ka fodya,” adatero Chakwera, ponena kuti atsutsa akuyesera kulepheretsa chitukuko cha dziko.
M’kutsiriza mawu ake, Chakwera anathokoza alimi a fodya chifukwa cha ntchito yawo yosalekeza ndipo adati: “Ogula fodyawa ndakamba nawo kale kuti akuguleni moona mtima.” Ndi mawu amenewa, iye anatsegula mwalamulo msika wa fodya wa chaka cha 2025.
Izi zikuwonetsa kuti boma la Chakwera lili pa njira yolimbikitsa makampani ofunika pa chuma cha dziko, ndipo alimi a fodya alandira chitsimikizo chothandizidwa komanso chithandizo pa msika wa 2025.
Follow and Subscribe Nyasa TV :