Chaponda akuti a Chakwera atulutse lipoti la Ngozi ya ndege ku Chikangawa
A George Chaponda, omwe ndi mtsogoleri otsutsa boma ku nyumba ya malamulo, wauza President Lazarus Chakwera kuti atulutse nsanga zotsatira za kafukufuku wa ngozi ya ndege yomwe idapha a Saulos Chilima ndi anthu ena asanu ndi atatu pa 10 June chaka chino.
A Chaponda ati a Chakwera adauza mtolankhani wa DW kuti akatswiri aku Germany adapereka lipoti la kafukufukuyu ku boma la Malawi. Koma nduna ya za mtengatenga a Jacob Hara yati palibe lipoti lotele kuchokera kwa akatswiriwa.
Naye mkulu wa nyumba ya malamulo a Richard Chimwendo Banda wati palibe lipoti lomwe akatswiriwa adapereka. Malingana ndi a Chimwendo Banda, akatswiriwa adangofotokoza moyepula ku boma komanso kubanja la a Chilima ndipo kuti lipoti la tsatanetsatane ngakhale boma silidalandire.
Apa, a Chaponda anafunsa ngati a Chimwendo Banda akutsutsana ndi zomwe a Chakwera alankhula.
A Chakwera adati lipotili alitulutsa likafika mu ‘ofesi zoyenelera’.