Chenjerani! Mlingo wa madzi wakwera kwambiri mu Lake Malawi

Nthambi ya boma yowona njira zotengera madzi ya National Water Resources Authority yati mlingo wa madzi mu nyanja ya dziko lino wakwera kwambiri chaka chino poyerekeza ndi zaka za m’mbuyomu.
Malingana ndi chikalata chomwe nthambiyi yatulutsa, mlingo wa madzi pofika pa 11 March chaka chino unali pa 475.95 meters omwe ndiokwera poyerekeza ndi mlingo wa madzi mu nyanjayi nthawi ngati yomweyi pomwe unali pa 475.12 meters.
Pamenepa, nthambiyi yati anthu omwe anakhadzikitsa ntchito za chuma komanso zaulimi mphepete mwa nyanja komanso magombe a dziko lino ali pachiopsezo chokumana ndi vuto lakusefukira kwa madzi.
Nthambiyi yapemphanso a Malawi kuti apewe mchitidwe omanga kapena kuchita ntchito za ulimi mphepete mwa nyanja pofuna kupewa ngozi zogwa mwadzidzidzi

Follow and Subscribe Nyasa TV :

Sharing is caring!

Follow us in Twitter
Read previous post:
Walusa! Chakwera adzudzula ma kampane a zomanga manga kamba kochedwetsa ntchito

Mtsogoleri wa dziko lino Dr Lazarus Chakwera wadzudzula ma kampane wena omwe amapatsidwa ntchito ya zomanga manga kuti akumachedwa kwambiri...

Close