Walusa! Chakwera adzudzula ma kampane a zomanga manga kamba kochedwetsa ntchito

Mtsogoleri wa dziko lino Dr Lazarus Chakwera wadzudzula ma kampane wena omwe amapatsidwa ntchito ya zomanga manga kuti akumachedwa kwambiri mukagwiridwe kawo ka ntchito.

Mukulankhula kwawo, a Chakwera adati ndiwokhumudwa ndi m’mene ntchito zina za chitukuko zikuchedwera mdziko muno.

A Chakwera alankhula izi lero boma la Rumphi komwe amatsekulira school zosula aziphuzitsi zomwe zamangidwa m’maboma a Rumphi, Mchinji komanso Chikwawa.

M’mawu ake mtsogoleri wa dziko linoyu adati ndizinthu zofunikira kwambiri kuti makontalikitala omwe apatsidwa ntchito azigwira ntchito yapamwamba komanso mwachangu kuti nzika za dziko lino zizikhutira kuti chitukuko chikupita chitsogolo.

Chakwera adapempha mlembi wa mkulu m’boma a collen Zamba kuti awonetsetsa kuti pali changu komaso kusintha pa m’mene ntchito za chitukuko zikuyendera.

“Dzulodzuloli ndimawadzudzula ma contractor ena ku Chitipa ndi ma official aboma amene agwira ntchito yomanga nsewu wina kumeneko mofowoka manja, ndipo ndawapatsa warning kuti zisapitilire.

Koma ma contractor amene mwagwira ntchito yomanga ma TTC amenewa, landirani ulemu wanu, chifukwa mwayitha. Ndiye Madam SPC amene muli pano, mwazionela nokha kuti ma contractor omanga zitukuko zosiyinasiyana mmaundunanso osiyanasiyana saakumagwira ntchito mofanana. Ndiye pilizi chonde, taonetsetsani kuti ntchito imuyenda mwa changu, ” adatero a Chakwera.

Follow and Subscribe Nyasa TV :

Sharing is caring!

Follow us in Twitter
Read previous post:
CSOs give Chakwera 7 days to own and explain the leaked Public Reforms Report

The CSOs, led by Charles Kajoloweka say the have noticed lack of transparency on the part of government to make...

Close