Chipani cha DPP chikuti a Chakwera ndi munthu wabodza lankunkhuniza

Chipani chotsutsa boma cha DPP chati mtsogoleri wadziko lino Lazarus Chakwera ndimunthu wabodza lankunkhuniza.

Navicha: 

Izi zadza pamene Chakwera lero anali mnyumba yamalamulo kuyankha mafunso a aphungu.

Poyankhula ndi MIJ Online, Mary Navicha mtsogoleri wa DPP mnyumba yamalamulo wati Chakwera zonse zimene wayankhula ndizabodza kamba koti anthu akugona ndinjala komanso ali paumphawi wazaoneni.

Navicha wati ngati Chakwera akufuna apite Madera monga akumudzi akaone mmene anthu akugonela madeya.

Follow and Subscribe Nyasa TV :
Follow us in Twitter