Chiwerengero cha anyama olemba JC chikutsika, pomwe cha atsikana chikukwerelabe
Chiwerengero cha anyamata amene akulemba mayeso a Form 2 chaka chino, chatsika ndi 7 percent pamene cha asungwana chikupitirira kukwera.
Izi zadziwika pamene wachiwiri kwa nduna ya za maphunziro, Nancy Chaola Mdooko, inayendera sukulu za Mchinji Secondary ndi Ngowe CDSS ku Lilongwe pamene mayeso a JCE ayamba lero.
A Chaola Mdooko ati palibe chosamwitsa chilichonse pamene mayesowa ayamba kamba koti boma linakonzekera ku mbali zonse zofunikira, kuphatikizapo chitetezo komanso malipiro a anthu oyang’anira mayesowa.
Ophunzira 163, 950 ndi amene akulemba mayeso a JCE chaka chino, ndipo asungwana alipo 84, 226 pamene chiwerengero cha anyamata ndi 79,724.
Chaka chatha asungwana analipo 90,434 komanso anyamata 85,998.