DPP igwedeza Zomba ndi uthenga wolimbikitsa anthu kuzavota: Khalani ndi chiphaso
Anthu ochuluka akuoneka m’malo momwe akuluakulu ena a chipani cha Democratic Progressive (DPP) akuchititsa misonkhano yomema anthu kuti akhale ndi chiphaso cha unzika.
Anthu ochuluka aoneka pa Thondwe, 6 Miles komanso kwa Mpunga m’boma la Zomba.
Pakadali pano, m’dipitiwu ukuthamangira mtunda wa kwa Namaraka, komwenso kuli anthu ochuluka.
Mwambo wa chipani cha Democratic Progressive Party (DPP) umene akuwutchula kuti DPP Parade, omwe cholinga chake n’kumema anthu kuti akonzenso chiphaso chawo cha unzika pokonzekera chisankho chapatatu cha chaka cha mawa, wayamba ku Zomba.
Mneneri wa chipani cha DPP, a Shadreck Namalomba, gavanala wa chipanichi ku chigawo cha ku mvuma, Sheikh Imran Ntenje, Phungu wa Zomba Malosa, Grace Kwelepeta, mkulu wa achinyamata ku chigawo cha ku mvuma, a Steven Bamusi, ndi ena mwa akuluakulu omwe ali nawo pa mdipitiwu.
Ulendowu, wayambira pa Thondwe ndipo ukathera ku Malosa, kwawo kwa a Kwelepeta.