Jetu wavuta! Dr. Joyce Banda akakamizidwa ndi azukulu ake kuti azivala ngati Jetu komanso apite ku ‘show’ yake
Kwavuta kunyumba kwa Dr Joyce Banda pomwe azukulu akakamiza mtsogoleri wa dziko lino wakaleyou kuti nayo azivala ngati woyimba Jetu komanso apite akawonere ‘show’ yake.

Nyimbo za celebu wamkulu, uja okwera ndege, Jetu, zikupitilira kukhala zachikoka kwa anthu amagulu onse, kuphatikizapo ana.
Pomwe president wakale Dr. Joyce Banda amacheza ndi adzukulu awo awiri dzulo, wina wa zaka 8 wang’ono kwambiriyo wazaka 5, adzukuluwo anawaphaphalitsa nawo mafunso agogo awowo, ngati akudziwa bwino za Jetu.
Anawa, mu nthawi yosakhalitsa, anatenga foni mkuwaonetsa agogo-wo (Dr. Joyce Banda), muja achitira Jetu; “Iwe ndi ndani?” Moti awaonetsa nyimbo zija anachina; Wakalamba wafuna komanso Chakwaza.

Dr. Joyce Banda, uku akungomwetulira; adzukuluwo sadasiyile pomwepo, awauza kuti aphunzire kuvina ngati Jetu, ayambe kutinta tsitsi ngati Jetu, komanso ayambe kuvala ma thalauza, mwinansotu Dr. Banda aphunzire kuvala chipewa, muja avalira Jetu-tu eti?
Ndiyetu president wakaleyu, moti pano walemba patsamba lake la Facebook kuti akufunitsitsa kuti, Jetu akabwera ku Lilongwe asaphonye show yake.
Follow and Subscribe Nyasa TV :