Joyce Banda wamema azimayi ophunzira mdziko muno kuti azitenga nawo pa ndale
Mtsogoleri wakale wa dziko lino mayi Joyce Banda alimbikitsa amayi ophunzira m’dziko lino kuti azitenga nawo mbali pa ndale.
A Banda anena izi lero ku University of Malawi (Unima) pa mkumano wa amayi amene ndi adindo a m’sukulu za ukachenjede komanso mabungwe osiyanasiyana m’dziko muno.
Iwo ati ku Nyumba ya Malamulo kumafunika atsogoleri amene azizukuta mfundo za chitukuko mwa ukadaulo bilo isanadutse osati kuvomereza zinthu zimene sakuzimvetsetsa.
“Ngakhale unduna umafunika atsogoleri amene maphunziro awo monga za umoyo, ulimi, za chuma ndi zina azifanana ndi unduna apatsidwawo chifukwa akuzidziwa mwakuya,” adatero iwo.
Malinga ndi Vice Chancellor wa Malawi University of Science and Technology (Must) mayi Address Malata, ati amayi amene akufuna kulowa ndalewa alowe pofuna kutumikira dziko osati m’matumba mwawo.
“Chofunikanso amayi tizitukulana osati kuponderezana,” adatero iwo.
Follow and Subscribe Nyasa TV :