Kabambe walonjeza kudzatsitsa Msonkho Wapamalipiro a Anthu Ogwira Ntchito [PAYE]

Mtsogoleli wa chipani cha UTM a Dalitso Kabambe ati anthu akawasakha pa udindo wa mtsogoleli wa dziko lino pa zisakho za pa 16 September adzayetsetsa kutsitsa ndalama ya msonkho yomwe anthu ogwila ntchito amapeleka ku boma malinga ndi momwe amalandila, Pay As You Earn (PAYE) pa chizungu.

Iwo ati anthu m’dziko muno kuphatikizapo ogwila ntchito komanso a zamalonda akufunyika, kukanika kutukuka chifukwa cha misonkho imene boma linaika yomwe-nso ndiyokwela kwambili.

A Kabambe ayakhula izi pomwe akupitiliza kuchita misokhano ya ndale m’boma la Lilongwe.

A Kabambe ati anthu muzintchito amaoneka ngati akulandira ndalama zambili koma pafupifupi theka la ndalama yawo, boma limatenga kukhala msokho, zomwe zikuchititsa kuti aMalawi ambili alephele kuchita zithu zatsogolo momasuka monga kumanya nyumba, kulipila sukulu zomwe zikupangitsa kuti ogwila ntchito ambili adzikhala mu ngongole.

“Tikalowa m’boma tidzatsitsa PAYE kufika pa 24.9% maximum komanso VAT pa 9.8% maximum, wa business tidzatsitsa msokho kuchoka pa 35% kufika pa 23.5% la phindu lomwe akupanga.

“Wa business, Boma likuchoka ndi 35% pa phindu lomwe wapanga posawerengela kuti yemweyonso walipira 16.5% VAT, yemweyonso walipira customs duty pa katundu wagula, kungoyerekeza kuti ugule galimoto kunja umagula galimoto yako, ina ya Boma, galimoto wagula MK3 million pa border Boma likutchaja MK5 million ngati msonkho. Dziko silingatukuke motero,” iwo anatelo.

Iwo anatsindika pokuti boma likuyenela kukhala ndi njila zambili zopezela chuma kupatula kuchokela ku misonkho.

“Vuto tili nalo, sitikupanga expand catchment area ya tax. Tikukama yomweyo yowonda osayipumitsa pamene ena dziko lomwelo saudziwa msonkho,” a Kabambe anatelo.

A Kabambe anati kukhala ndi njila zambili zopezela chuma ngati dziko kudzathandiza kuti zithu zambili zitsike mitengo mbali inayi zidzapeleka danga kwa ma kampani kupanga ntchito zochuluka kwa anthu popeza adzakhala kuti ayamba kuona mphindu lochitila malonda m’dziko muno.

“Boma lathu lidzakhala ndi ntchito yopanga create ma millionaire atsopano omwe adzakhala akupereka misonkho komanso mbali zina za business m’misika yathu tidzaonetsetsa kuti akupeleka ka msonkho koyenera ndi business yawo, kuli ma business ambili omwe sapereka misonkho koma akupanga phindu lochuluka, nkwabwino kupereaka ambili koma mochedwa kulekana nkupereka ochepa koma azipereka kwambili,” iwo atsindika.

Follow and Subscribe Nyasa TV :
Follow us in Twitter

Leave a comment

Your email address will not be published. Required fields are marked *