Kabambe watsimikizila anthu ku Mchinji za ubwino oyika anthu odziwa ntchito m’malo mwake

Mtsogoleli wa chipani cha UTM a Dalitso Kabambe wauza anthu m’boma la Mchinji kuganizila zoika m’maudindo atsogolela oyenelela kugwila ntchito zokweza chuma cha dziko lino pomwe chisankho chikuyandikila.

Pa misokhano yawo yokopa anthu yomwe anali nayo m’bomali a Kabambe atsindika kuti ntchito yoyendetsa dziko sifuna munthu ophunzilila koma yemwe ali ndi kuthekela kale.

“Dzulo, tinakambirana za ubwino olemba munthu ntchito yemwe ali ndi maphunziro ogwirizana ndi ntchitoyo, koma sizimathera pompo, timayeneranso tione experience yake kuti asatichedwetse ndi gwirugwiru komanso training, pa chizungu amati “hands-on-experience”. Mukatenga munthu wa hands on experience sakutayitsani nthawi, komanso sadalira ena kuti amugwilire ntchito, kaya ndi engine ya galimoto amagwetsa yekha, hands-on- experience,” Kabambe anatelo.

Iwo anatsimikizilanso anthu-wa zakuthekela komwe ali nako poyendetsa chuma ponena kuti kaundula wa momwe anagwilila ntchito amaonetselatu kuti iwo anagwila ntchito-yi mwaukadaulo.

“Moyo wanga onse ndagwira ntchito ya zachuma. Ntchito zolodzeka, record yoti mutha kukayilondoloza. Zitha kutheka kuti ndimagwira ntchito pansi pa President wina, komabe, impact ya udindo uliwonse imatha kuwunikiridwa pa yokha,” iwo anatelo.

Iwo anapitilizanso pofotokoza momwe anakwanitsila kutukula kayendetsedwe ka chuma ku Banki yaikulu ya Reserve;

“Mwachitsanzo, ku Reserve Bank ndinapita mu 2017. DPP inalowa m’boma 2014. Koma pomwe ndimapita ku Reserve Bank ndinapedza record yoti Reserve Bank inkapanga ma loss. Inflation inali ili pa 22% ndipo ma interest rates anali okwera, pansi pa ulamuliro wa Professor Mutharika, chipani cha DPP. Nditafika ku Reserve Bank ndinapanga kauniuni wanga, mu luntha ndi mzeru zanga ndinapanga detect zofunika kukonza, zomwe ndinali ndi mphamvu zokomza, ndinakomza. Ndipo mu chaka chomwecho inflation inatsika kufika pa 18% ndipo tinapanga post K7 billion profit, from poised losses.

“Sindinalekere pomwepo, ndinagwira ntchito molimbika kulimbana nayo stability ya kwacha, kwa zaka zinayi ndinali ku Reserve Bank ndinayipeza Kwacha ili pa K732.40 to 1 dollar mu 2017 ndipo ndinayisiyanso ili pa K732.40 to 1 dollar, outstanding,”

Mukufotokoza kwawo a Kabambe anafotokozanso momwe anakwanitsila kukweza mphamvu ya ndalama ya kwacha komanso kupanga kuti dziko lino lidzikhala ndi ndalama zochuluka za maiko ena ija amati Forex pa chizungu.

“Nayo inflation ndinatsitsa kuchoka pa 22% mu 2017 kudzafika pa 7% mu 2020 pomwe ankandichotsa. Forex cover ndinapedza ya 2 weeks in 2017, ndipo ndinasiya ma dollars ambirimbiri okwanira miyezi 6 mu 2020. Interest rates ndinayipeza ili yokwera, around 20%, ndinayitsitsa kufika pa 12% only,”.

Iwo anati izitu zinachitika kaamba ka ukadaulo wawo potengela kuti ngakhale chipani cha DPP chinali mu ulamulilo dzaka zoyambilila zithu sizimayendabe bwino kufikila iwo atakhala wamkulu wa Banki ya Reserve.

Ndipo iwo anamaliza ndikuuza anthu-wa kuti sakupepha voti ndicholinga chifuna kudzawatayitsa thawi koma kuti akufuna kudzakonza mavuta a kusowa kwa ndalama ya maiko ena, umphawi, njala komanso kuti za malonda zidzayambe kuyenda bwino.

Follow and Subscribe Nyasa TV :
Follow us in Twitter