Khansala wa DPP wazitaya ku Mzimba Hora, walowa chipani cha Aford

Khansala wa dera la Mzalangwe ku Mzimba Hora, a Dani Nkosi watuluka chipani cha DPP ndipo walowa chipani cha AFORD.

Poyankhula atalandiridwa ndi akuluakulu achipani cha AFORD, Nkosi wati walowa chipanichi ndicholinga choti chigawo chakumpoto kwa dziko lino nako kukhale chipani champhamvu.

A Nkosi ati izi zichititsa kuti chigawo chakumpoto chikhale ndi zitukuko zolozeka monga m’mene ziliri madera ena.

M’mawu ake, wapampando wa chipani cha AFORD kuchigawo cha Mombera, a Staford Bondera Nyirenda wati chipani cha AFORD chikukula ndipo anthu ambiri akhale akulowa mchipanichi mtsogolomu.

Chipani cha AFORD chiri ndi aphungu awiri ku nyumba ya malamulo ndipo aphunguwa ndi aku Mzimba.

 

Follow and Subscribe Nyasa TV :

Sharing is caring!

Follow us in Twitter
Read previous post:
Witness tells court that late Witika was dating several women including ‘certain three women.’

The fourth state witness in the Allan Witika murder case, Andrew Mdala, testified in court on Wednesday and during cross-examination,...

Close