Khonsolo ya Lilongwe yayamba kugwesa ma shop omangidwa malo osalolezedwa m’muzindawu

Khonsolo ya mzinda wa Lilongwe m’bandakucha wa lero yagwetsa nyumba zomwe anthu ena anamanga ku Malangalanga mu mzinda wa Lilongwe.

Malingana ndi mneneri wa khonsoloyi a Tamara Chafunya, nyumba zina zomwe eni ake anatenga chiletso ku khothi kuti asawagwetsere, azisiya kaye pakadali pano.

Iwo ati ntchitoyi akhala akuyigwira m’malo ochitira malonda komanso okhala anthu, ngakhale anthu akhala pamalopo kwa zaka zoposa 20, koma nyumbazo azigwetsa ndithu.

M’modzi mwa akuluakulu a bungwe la eni minibus m’chigawo cha pakati a Herman Msowoya wati ndalama zoposa 150 million kwacha zalowa m’madzi, ndipo wadandaula kuti sanawapatse mpata wokonzekera, ngakhale kuti anaagwirizana kuti adzachita izi pakapita masiku 29.

Winanso a Alfonso Jamali womwe amagulitsa zitsulo za galimoto wadandaula kuti 600-million-kwacha zalowa m’modzi pa nyumba 60 zomwe azigwetsa, ndipo adandaula kuti khonsolo ikukondera pogwetsa sitolozi, popeza mzika za mayiko ena monga Nigeria ndi India, ngakhale Amalawi ena, sanazigwetse.

 

Follow and Subscribe Nyasa TV :

Sharing is caring!

Follow us in Twitter
Read previous post:
Malawi’s ‘first professional tattoo studio’ set to open in Lilongwe

Tattoo enthusiasts in Malawi now have a reason to be more excited as Black Flame Ink, the “first professional tattoo...

Close