Mabungwe à CHRR ndi MACODA a kulimbikitsa anthu aulumali kudziwa Ufulu wawo bwino,kutsatira zisankho
Bungwe lomenyera Ufulu wa anthu omwe ali ndi ulumali wosiyanasiyana la CHRR mongwirizana ndi bungwe loyang’anira mabungwe ena pa nkhaniyi, la MACODA likuchititsa mkumano wounikira anthuwa pa ufulu omwe amawalora kulumikizitsidwa bwino lomwe pa nkhani ya zisankho ndi muzipani za ndale m’dziko muno.
Mkumanowu womwe ndi wamasiku awiri ukuchitikira mu mzinda wa Blantyre wayamba lachisanu ndipo ukuyembekezereka kutha loweluka lino.
Mabungwe onse okhudzidwa m’dziko muno ali nawo pa ma phunzirowa.
Ena mwa mabungwewa ndi monga owoona za anthu omwe ali ndi khungu la chiaulubino,owona za anthu omwe ali ndi vuto la Maso komanso kusamva ,mwa ochepa chabe.
Payakhula potsegulira maphunzirowa ,mmodzi mwa akulu akulu oyendetsa ntchito za bungwe la CHRR a Maxwell Mvula wati ,pali magawo ena pomwe anthu pomwe ali ndi ulumali wosiyanasiyana sadziwa bwino ndipo izi zimapeleka mwayi kwa anthu ena kuti azipondereza anthuwa mu zambiri.kotero maphunzilowa awatsegula maso.
“Munthu waulumali naye ali ndi ufulu wowelengedwa pasisankho,muzipani za ndale popatsidwa chisamaliro komanso udindo wina uliwonse malingana ndi kuthekera kwake pa ntchito”
“Koma zimamvetsa chisoni anthuwa akakhala kuti sakudziwa zambiri za ufulu wawo akadziwa izi ziwachitira ubwino muzambiri” Watero Mvula.
A Mvula anatinso achita izi maka polingalira kuti zina mwa nkhanizi zikukhudzanso ufulu wolumikizitsa anthuwa mu ndondomeko zoyendetsera zisankho kuti nawo anganizilidwe moyenerera Malingana ndi malamulonso a m’dziko lino.
Mkulu wa bungwe loyang’anila mabungwe ena onse okhudzidwa pa nkhaniyi la MACODA,George Chiusiwa wati bungweli wamemeza anthu omwe ali ndi ulumali kuti adzikhàla ndi chidwi powelenga malamulo oyendetsera dziko komanso malamulo akhudza umoyo wawo kuti asamaponderezedwe mu zinthu zambiri popheredwa ufulu.
“Ukhakhala osadziwa ufulu wako anthu amakupezerera muzambiri posakuwerengerani mu zinthu zambiri, mukuyenera kumawelennga malamulo onse kuphatikizapo zokhudza za kuyendetsedwe Ka dziko,mokatero mukhala mfulu weniweni” atero a Chiusiwa.
Iwo atinso akhala akuchita zokambirana ndi mabungwe monga loyendetsa zisankho la MEC kuti athe kuunikirana zina mwa zomwe zikuyenerabe kuti ziunikilidwebe zokhudza anthu omwe ali ndi ulumali mdziko muno potengera kuti tsiku la zisankho layandikira m’chakachi.
“Pali zinthu zina zomwe tikukambiràna ndi a MEC zomwe tikuyenera kuziunikiràbe zokhudza kasamalidwe,kulumikizitsidwa mu mmaudiñdo ndi zipani za ndale pakati pa anthu omwe ali ndi ulumaliri wosiyanasiyana monga mu chiwerengero cha omwe akulembetsa mu ndale popeleka ndalama yochepelepo pomwe ati chiwelengero chenicheni zichikutsatidwa bwino ,mwa zina” anayankhula motero a Chiusiwa.
Ndipo m’mawu ake Smart Vinti yemwe ndi wakhungu la chiaubino anati izi zawalimbikitsa ndipo kuti Maso awo atseguka tsopano.
Follow and Subscribe Nyasa TV :