Nditukula Malawi mosatengera chigawo, mtundu wa anthu – Chakwera

Pulezidenti Lazarus Chakwera watsimikizira a Malawi kuti boma lake lipitiriza kupereka zitukuko mosatengera chigawo kapena mtundu wa anthu.

Polankhula m’boma la Rumphi pomwe amatsegulira sukulu zitatu zosula aphunzitsi m’maboma a Chikwawa, Mchinji ndi Rumphi, Chakwera anati ndi cholinga cha boma lake kuti dera lililonse lilandire chitukuko mofanana.

Mtsogoleriyu anati ichi ndi chifukwa chake boma lake lawonjezera ndalama za mthumba la chitukuko la Constituency Development Fund (CDF) kuchoka pa K100 miliyoni kufika pa K200 miliyoni.

“Ndichifukwa chake m’maboma onse m’dziko muno tikulimbikitsa ntchito zotukula madela onse. Panopa mu Constituency iriyonse m’Malawi muno mukumangidwa zitukuko zosiyanasiyana chifukwa cha ndalama zomwe ndakhala ndikuika mu ma Constituency Development Fund onse, ndipo chaka chino ndaonjezeranso ndalama zina muthumba limeneli. Oti olo a MP adela lanu akhale achipani china, mukuyenera kumawafunsa kuti kodi ndalama ya CDF yomwe a Pulezidenti akumakupatsani mwamangila chani?” anatero a Chakwera.

“Ndipo ngati ali achilungamo, akuuzani kuti ndalama yomwe boma la aChakwera latipatsa ndizomwe zakubweretserani biriji iyi, police station iyi, sukulu iyi, nsewu uwu, district office iyi, stadium iyi, kapena magetsi awa. Ndapanga zimenezi mosasankha chigawo, kapena mtundu, kapena chipani, chifukwa ntchito yotukula madela onse a m’Malawi kuti tonse titukukire pamodzi ndi ntchito yomwe ndinalonjeza komanso yomwe a Malawi munandituma. Ndipo m’Malawi muno mulibe MP olo mmodzi amene anganene kuti sindinafikitse chitukuko m’dela mwake, chifukwa chitukuko chiri chonse chomwe angaloze kuti iyeyo wabweretsa mu Constituency mwake, ndalama zopangira chitukukocho ndinapereka ndi ine. Ndiye mukaona MP akuloza chitukuko m’dela lake chomwe chatheka ndi Constituency Development Fund, dziwani kuti zitukuko ndinalonjeza zija zikutheka,” iwo anawonjezera motero.

Koma Chakwera anatsindika kunena kuti kutukula madera onse mokwanira kapena kutukula miyoyo ya a Malawi onse ndi umoyo wabwino zitha kukhala chabe ngati boma silikuwapatsa maphunziro ndi maluso omwe angathandize Amalawi kudzitukula okha.

Iwo anati gawo lotukula kuthekera kwa munthu ndi lofunikira kwambiri kaamba koti ndi gawo lomwe limamupatsa munthu ukadaulo womuthandiza kuti azidziyimira payekha, komanso ndi gawo lomwe limampatsa munthu ufulu womwe amasowa kuti akhale wodzidalira.

“Ndiye kuthekera kumeneku kumabwera ndi maphunziro abwino, chifukwa kuphunzira bwino si sukulu koma kaphunzitsidwe. Ndiye lero ndine okondwa kudzatsekulira ma Teacher Training College atatu amene tamaliza kumanga mzigawo zonse zitatu, imodzi kum’mwera ku Chikwawa, imodzi pakati ku Mchinji, imodzi kumpoto kuno ku Rumphi, ndipo onsewa ali ndi ma labu a makompyuta kuti aziphunzitsi azidziwa kuphunzitsa ana munjira zamakono.

“Izizi ndizimene ziri mmasomphenya adziko lathu a Malawi 2063, makamaka pansanamira yachinayi ya Human Capital Development. Ndiye ine ndiothokoza kwa abale athu amayiko akunja amene mwatithandiza kuti zimenezi zitheke, abale ngati a BADEA, the Saudi Fund for Development, ndi a OPEC Fund for International Development. Komanso ndithokoze ma contractor pantchito yotamandika yomwe mwagwira mwayigwira,” anatero mtsogoleriyu.

Follow and Subscribe Nyasa TV :

Sharing is caring!

Follow us in Twitter
Read previous post:
Long walk to justice as Bushiri extradition hearing pushed to May 15

The extradition case on Shepherd Bushiri and his wife Mary has been adjourned to 15th May, 2024 when the defense...

Close