Nthambi ya za nyengo yikuti mchigawo chakumwera ndi pakati anthu ayembekezere mvula yambiri kuyambira lero

Nthambi yoona za nyengo ndi kusintha kwa nyengo yati madera a mchigawo chakumwera komanso pakati pa dziko lino ayembekezere mvula ya mphamvu komanso ya mabingu kuyambira m’mawa uno kufikila Lachisanu likudzali.

Mvulayi ati ikhala ya mphamvu kaamba ka dera lozetsa mvura lotchedwa ITCZ.

Izi ndi malingana ndi ulosi wamomwe nyengo ikhalire kuyambira lero mpaka pa 3 March womwe nthambiyi yatulutsa.

Mwazina, nthambiyi yachenjeza za chiopsezo cha kusefukira kwa madzi m’madera amphepete mwa nyanja ya Malawi monga Karonga, Salima komanso madera otsika chifukwa cha chamvulayi yomwe ati ikhala ya mphepo ndi mabingu.

Msabata ziwiri zangothazi, kwakhala kuli ng’amba komanso mvula yochepa m’madera ambiri akummwera komanso pakati pa dziko lino zomwe zakhudza alimi ambiri popeza mbewu zawo zikuwuma.

 

Follow and Subscribe Nyasa TV :

Sharing is caring!

Follow us in Twitter
Read previous post:
Rotary Club of Lilongwe-Lingadzi on mission to plant 100, 000 trees

Rotary Club of Lilongwe-Lingadzi President, Giorgia Prizzon said her club is on a mission to plant 100, 000 trees in...

Close