Salary K52000 thumba lachimanga K50 000? Adabwa ogwira ntchito zapakhomo pokana zomwe boma lakhazikitsa

Ogwira ntchito za pakhomo komanso m’mashopu ati ndi chitonzo chachikulu chomwe boma lapanga chifukwa iwowa amagwira ntchito yambiri ndipo ati n’zomvetsa chisoni kuona boma likufananiza malipiro awo ndi thumba limodzi la chimanga.

Izi ogwira nthitowa anena mu mzinda wa Lilongwe  pomwe anachititsa msonkhano wa atolankhani poonetsa kusakondwa ndi ganizo la boma pa malipiro a anthu ogwira ntchitozi.

Iwo ati malipiro a omwe akugwira ntchito m’mashopu achoka pa K50,000 kufika pa K90,000 ndipo omwe akugwira ntchito za pakhomo achoka pa K38,000 kufika pa K52,000.

Mtsogoleri wa bungwe la ogwira ntchitowa a Jafali Abdul ati iwo salola malipiro omwe boma lakhazikitsawa.

“Ife salary K52,000, thumba la chimanga K50,000. Mwina K2,000 ayika kuti yogayitsira, komanso siyingakwane chilichonse chakwera mtengo. Kodi ogwira ntchito m’nyumba ndi mu shop si munthu? Ifeyo sitikumvetsani chisoni?” Atero a Abdul.

Iwo aopseza kuti achita zionetsero ngati boma silisintha chiganizo chake pa malipiro awo.

“Tiwajoyina ma truck drivers.”

Follow and Subscribe Nyasa TV :

Sharing is caring!

Follow us in Twitter
Read previous post:
Germany provides €16m for 3rd phase of Reproductive Health Pogramme in Malawi

Germany has provided a whopping €16 million (approximately MK30 billion) to enable Malawi implement the third phase of the Programme...

Close