Simbi apempha a Malawi: Chilima sanali waziwawa, sanali wamabodza, tiyeni timulemekeze

Mmodzi mwa anthu odziwika pa nkhani za mabizinesi akulu mdziko muno a Simbi Phiri apempha a Malawi kuti alemekeze malemu Saulos Chilima poleka kufalitsa nkhani zamabodza, miseche, kutukwanana, zipolowe komanso kuyika zithunzi zosakhala bwino pamasamba a intaneti.

Simbi Phiri: 

Poyankhula ndi atolankhani lero, a Simbi—omwe ati amawaziwa bwino a Chilima—ati a Malawi ambiri asauka nayo imfa ya a Chilima ndipo tonse tivolemeleze kuti maliro awa abwere moyipa.

“Mkhalidwe womayankhula zinthu zoti anaphedwa motere, adamchitika ndi wakuti pomwe ukudziwa kuti ukunama, sibwino. Muwonongetsa dziko. Dziko lathu lili mmavuto kale, ndiye kuti tiziyankhula zotero tiyika mitima ya anthu mumulengalenga,” atero a Simbi.

Iwo atinso ngati sitisamala anthu ayamba kuphana, kuthyolerana katundu mdziko muno.

“Mkhalidwe wotero siwabwino. Munthu aliyense yomwe ali ndi ma picture a Chilima, musawayike pa intaneti. Ndichipongwe. Mukumunyoza iyeyo. Ngati muli ndi ulemu ndi Saulosi, pepani anthu akwathu musatero ayi,” atero a Simbi.

Pakali pano ma lipoti akuti ku Ntcheu anthu akugenda magalimoto odutsa mu nsewu.

Follow and Subscribe Nyasa TV :
Follow us in Twitter