Tobias akumbutsa aMalawi za kufunikira kovotera mtsogoleri wangwiro komanso wa masomphenya
Yemwe akufuna kudzayimira nawo pa mpikisano wa mtsogoleri wa dziko, a Milward Tobias, alangiza aMalawi za kufunikira kosankha mtsogoleri wa masomphenya komanso luntha ndi chidziwitso pa mmene chuma cha dziko chikuyendera.

Ndipo a Tobias – yemwe ndi mkadaulo pa nkhani za chuma – ati iwowo ndi munthu yekhayo yemwe pakali pano wadzipereka kudzatumikira dziko lino mwa ungwiro, ukadaulo pofuna kutukula chuma ndi miyoyo ya anthu molingana ndi kuthekera kumene dziko lino liri nako.
Iwo ati pofuna kukwaniritsa izi, iwo adzakonza pulani yomveka bwino ya chitukuko cha dziko ndi miyoyo ya anthu, komanos kukhala ndi danga labwino lowathandizira kuti akwaniritse masomphenya ndi malonjezo awo
“Ena mwa amene tidzapikisane masomphenya ali nawo. Chimene sadzakhala nacho ndi danga labwino. Danga ili lingapezeke pokha pokha titachotsa magoli awiri amene amapangitsa atsogoleri a ndale kuoneka a nzeru ndi opereka chiyembekezo asanalowe m’boma koma kukaononga chuma cha boma ndi kuzunza anthu akangolowa m’boma,” anatero a Tobias mkucheza ndi Nyasa Times Lachisanu.
Iwo anati magoli amenewa alipo ndi monga ndale za chipani, zimene zimapangitsa wopikisana pa chisankho kugwiritsa ntchito ndalama pokopa anthu.
A Tobias anati vuto lalikulu logwiritsa ntchito ndalama pokopa anthu ndi loti andale amakakamizidwa kukatenga ndalama kwa akambelembele ndi anthu adyera kumagula zitenje, zovala, zipewa ndi galimoto pamene ndalama zina amagawa kwa anthu mmisonkhano yokopa anthu.
“Zitsanzo ziwiri zowonetsa umboni kuti tikachotsa magoli awa ndikukhala ndi mtsogoleri wa masomphenya ndi wodziwa kuyendetsa chuma dziko lino lipita patsogolo nazi: President Ibrahim Traore wa dziko la Burkina Faso alibe chipani ndipo sadakhale president pochita misonkhano yokopa anthu. Chifukwa cha ichi, ziganizo zake zimakhala zoyang’ana fuko la dziko osati mmene anthu ena adagwirira ntchito yokopa anthu kuti amuvotere kapena ndalama zimene adapereka kuthandiza kukopa anthu. Iye alibe magoli amenewa.
“Malemu president professor Bingu wa Mutharika teremu yawo yoyamba. Atatuluka chipani chimene adali nthawi ya chisankho cha 2004, adakhala mtsogoleri opanda chipani ndipo ngati kunali makhuluku ndi anthu adyera opereka ndalama ndi katundu wochitira misonkhano yokopa anthu ndi cholinga choti chipani chikawina chisankho iwo adzapindule, anthu amenewo amadziwana ndi amene adali atsogoleri a chipani pa nthawiyo osati malemu president professor Bingu wa Mutharika chifukwa iwo anali ngati mulendo mu chipanicho. Izi zidapangitsa kuti akhale ndi danga labwino lotsogolera a Malawi onse chimodzimodzi popanda gulu lina lomadzimva kuti ndi anthu ofunika kuposa ena chifukwa ali mbali yolamula. Chidwi chawo chonse chinali kuyendetsa dziko, kutukula miyoyo ya anthu osati chidwi chogawanikana pakati poyendetsa dziko ndi kuyendetsa chipani. Chuma chidakwera mofulumira, njala idatha, mitengo ya katundu inali yokhazikika. Atapanga chipani, tonse tikudziwa mmene zinthu zidasinthira,” anofotokoza chonchi a Tobias.
Zinanso zimene anatsindikapo pa kulankhalana kwathu ndi izi:
“Ndakhala ndikunena kuti aliyense amene adzaime mu dzina la chipani sikusintha kumene tikukufuna. Aliyense amene akukopa anthu pogawa nsalu, ma t-shirt, ndalama ndikumayenda pa mdipiti wa galimoto zambirimbiri mudziwe kuti watipangitsa pinyolo kwa zigawenga.
Kuli anthu ku mbuyo kwake amene akupereka ndalama kuti akakhala pa mpando adzikawapatsa mwayi wa bizinezi za boma mowakondera pa mtengo wokwera kwambiri ndalama zonse nkumasakazika ife tikusowa zipangizo za ulimi zotsika mtengo, madzi akumwa abwino, mankhwala ku chipatala, miseu yabwino ndi zina.
Palibe ngakhale mmodzi wa amene akupanga ndale angakwanitse njira zokopa anthu mumazionazi. Ngati alipo muwafunse ndalama adazitenga kuti? Pakadali pano anthu amene alembetsa kudzavota ndi 7.1 million. Mongoyerekeza kugawa nsalu 3 million iliyonse mtengo wake K5000 pafunika K15 billion. Kugawa ma t-shirt 3 million iliyonse mtengo wake K5000 pafunikanso K15 billion.
Kuthetsa katangale sikungatheke ngati njira yopitira mu ofesi yathandizidwa ndi katangale yemweyo. Kuthetsa katangale kukufunika mtsogoleri apite mu ofesi alibe goli lirilonse.
Kusintha kwenikweni ndi kumene ndikubweretsaku. Tachotseratu magoli awiri amenewa. Ine ndakonzeka kukutumikirani mwa ungwiro, ukadaulo ndi modzipereka.
Thandizani kusintha kwenikweni pogawa uthengawu kwa anzanu kuti ufikire anthu ambiri.”
Follow and Subscribe Nyasa TV :