Tonse Alliance ndi ya bodza: Palibe akudya katatu mu Malawi muno, atero a Bright Msaka

Bright Msaka yemwe ndi phungu wa DPP ku Machinga Likwenu wati anthu ambili mdziko muno sakukwanitsa kudya katatu monga momwe zimayenera kukhalira malingana ndi malonjezano omwe boma la mgwirizano wa Tonse lidalonjeza a Malawi mmbuyomu.

Izi zanenedwa  pomwe aphungu akupitirizabe kuikapo ndemanga zawo pa ndondomeko ya za chuma ya chaka chino yomwe inaperekedwa ku nyumba ya malamulo ndi nduma yaza chuma Simplex Chithyola Banda.

Malingana ndi Msaka anthu ochuluka akuvutika mdziko muno kamba ka kukwera mitengo kwa katundu osiyanasiyana pa msika kutsatira kugwetsedwa mphamvu kwa ndalama ya Kwacha.

Mwazina Msaka wati boma la Tonse lalepheranso kuthana ndi mavuto akusowa kwa mankhwala  mzipatala komanso mavuto akusowa kwa zipangizo zokwanira zophunzirira msukulu za mdziko muno.

Mmawu, ake Msaka wati boma la Tonse silikuchitapo kathu kuthana ndi mavuto a njala mdziko ndipo lawataya a Malawi kufika poti mpaka aneneri komanso abusa ndi omwe akukwanitsa kugawa chimanga ntchito yomwe ati imayenera kugwiridwa ndi unduna wa za ulimi ngati udindo wa boma.

Koma poyankhapo ku mbali ya boma pa nkhani yi nduna yaza umuyo Khumbize Kandodo Chiponda wati sikoyenera kunena kuti boma silikuchita po kanthu poti boma likuchita zonse zothekera kufuna kuthana ndi mavuto anjala komanso aza chuma mdziko muno.

Follow and Subscribe Nyasa TV :

Sharing is caring!

Follow us in Twitter
1 Comment
newest
oldest most voted
Inline Feedbacks
View all comments
Galugalu
7 months ago

Nanga ife popeza tikudya kanayi Pali vuto ngati ?

Read previous post:
Prophet Gama says socialite Pemphero Mphande will one day be Malawi’s president

One of the renowned men of God in the country Prophet Awesome Gama has prophesised that socialite Pemphero Mphande will...

Close