UTM ikuti mgwirizano wawo ndi MCP ukadali chimodzimodzi

Chipani cha UTM chati mgwirizano wawo ndi MCP pa yemwe akudzaimira mgwirizano wa Tonse mu chisankho chikudzachi sudasinthe ndipo ‘udakali chimodzimodzi’.

Mlembi wamkulu wa UTM, Patricia Kaliati, watiuza kuti adagawana zaka zisanu kwa otsogolera aliyense ndipo kuti mfundoyi sidachitike ndi atsogoleri a zipani ziwiri zokhazi ayi koma kuti otsatira ena adavomereza.

Malingana ndi Kaliati, mgwirizanowu ukudzaimiliridwa ndi mtsogoleri wa UTM, Saulos Chilima, pa chisankho cha chaka cha mawa popeza kuti mtsogoleri wa MCP, Lazarus Chakwera wachita kale mbali yake.

Izitu zikudza patapita sabata komiti yaikulu ya MCP itanena kuti odzaimila chipanichi mu chisankho chikudzayi ndi President Chakwera.

Poyankhurapo, katswiri pa ndale George Phiri wati kusainila mgwirizano kwa atsogoleri a mu mgwirizano wa Tonse kumaimila zipani zawo ndinso kuti MCP kusakha mtsogoleri wawo mu 2025 kukhoza kukhala mbali imodzi yokwaniritsa za mgwirizanowu.

Follow and Subscribe Nyasa TV :

Sharing is caring!

Follow us in Twitter
Read previous post:
Prophetess Kambale donates foodstuffs to elderly people in LL’s Area 26

Prophetess Petite Kambale – a wife of the renowned founder of Life International Church, Prophet Amos Kambale – over the weekend made...

Close