Woyimba Maskal wafika mudziko muno Kuchoka USA kuzayimba ku Chiphwando ku Illusionz loweluka

Woyimba wodziwika bwino Maskal, yemwe akukhala m’dziko la United States of America wafika m’dziko muno kudzera ku bwalo la ndege la Kamuzu mu mzinda wa Lilongwe.

Maskal, yemwe amadziwika ndi nyimbo zake monga ‘Udalire’, akuyembekezeka kukhala nawo pa phwando la maimbidwe ku Illusionz mu mzinda wa Lilongwe Loweruka.

Phwando la maimbidweli likusangalalira Nde’feyo Entertainment yomwe inatenga chikoka m’mbuyomu ikugwira ntchito ndi oyimba monga Maskal, Onesimus komanso Piksy.

“Tafika basi tiyipatse moto. East or West home is best. Tipange zinthu,” anatero Maskal yemwe akhale akukumana maso ndi maso ndi Onesimus komanso Piksy.

Phwandoli likuyembekezeka kuchitikanso mu mzinda wa Blantyre.

Nde’feyo Entertainment idayambitsidwa ndi Khumbo Kabuzi Munthali yemwenso akukhala ku America komanso Zizwa yemwe dzina lake lenileni ndi Ken Limwame.

Follow and Subscribe Nyasa TV :

Sharing is caring!

Follow us in Twitter
Read previous post:
Chakwera rejects bill that would have made Malawians fund political party campaigns

President Lazarus Chakwera has refused to sign into law an amendment in the Political Party Act which sought to oblige...

Close