Zoopsa! Amangidwa kamba kotsatsa malonda a mwana womupeza wa zaka ziwiri

Apolisi m’boma la Zomba amanga a Chimwemwe Zololo chifukwa chofuna kugulitsa mwana wao wamwamuna omupeza wa zaka ziwiri.

Wachiwiri kwa mneneri wa a polisi m’bomali a Aaron Chilala ati a Zololo amatsatsa malonda a mwanayo kwa mpondamatiki wina amene amachita malonda osiyanasiyana m’bomali.

Malinga ndi a Chilala, mpondamatikiyu adatsina khutu apolisi za nkhaniyi ndipo apolisiwa adalangiza mkuluyu kuti avomere za malondawo kuti apolisiwa apeze mpata odzagwira bamboyu.

Chilala adati awiriwa  adagwirizana kuti akumane 4 koloko masana ku nyumba kwa chikhwayacho kumene apolisiwa adamyata kuti amugwire mkuluyu.

“Mkuluyu atafika ndi mwanayo adayamba kukambilana ndi chikhwayacho za mtengo umene angagulire mwanayo ndi pamene apolisi adavumbuluka ndi kumumanga,” adatero Chilala.

Chilala adapitiliza kunena kuti apolisiwa adayitanitsa mkazi wa mwamunayu amene adavomera kuti bambowa adanenadi maganizo awo ogulitsa mwanayo pofuna kuthana ndi mavuto a zachuma amene banja lawo likudutsa koma mkaziyo adakana.

A Zololo amene amachokera m’mudzi wa Chimbalanga mdera la mfumu yaikulu Chiwalo m’boma la Phalombe, akuyembekezera kukawonekera ku bwalo la milandu kukayankha mulanduwu.

Follow and Subscribe Nyasa TV :

Sharing is caring!

Follow us in Twitter
Read previous post:
PRISAM SACCO gears to ease private schools financial burdens

Newly elected Private Schools Association of Malawi (PRISAM) executive has said apart from ensuring that schools registered under the association...

Close