A Mutharika achezera Asilamu pa Mzikiti wa Mangochi main, agawa zakudya zambiri

Mtsogoleri wakale wa dziko lino yemwenso ndi Mtsogoleri wa Chipani cha Democratic Progressive Party-DPP, His Excellency Professor Arthur Peter Mutharika, lero chakusanaku anakachezera asilamu pa Mzikiti wa Mangochi Main Mosque ntown ya Mangochi.

Mwachizowezi, a Mutharika anachezera komanso kuwalimbikisa abale ndi alongo achisilamu amene padakali pano ali mu nyenyo Ramadan. Iwo ananena kuti nyenyo ya Ramadan ndi yofunikira kwambiri imene ili nthawi imene otsatira chipembezo Cha chisilamu amayandikana ndi Allah posala kudya, komanso kuchita ntchito zachifundo (Zakaati).

Pofuna kuwonetsa chikondi chawo, A Mutharika agawa zakudya monga mpunga, sugar komanso ufa zoti anthu pa mzikitipa azigwiritsa ntchito amakamasula Ramadan.

Paulendowu, Iwo anaperekezedwa ndi Olemekezeka Sameer Suleman MP, olemekezeka a Ralph Jooma, Sheik Salire Saidi komanso akulu akulu ampingo wa chisilamu m’bomali.

Poyankhulapo, mmodzi mwa akuluakulu a chipembedzo cha chisilamu womwe anali nawo pa mwambowu anati Professor Mutharika wakhala akuchita izi chaka ndi chaka ndipo asilamu wonse ku Mangochi ndiwokondwa chifukwa akawona Professor Mutharika akuwayendera amalimbikitsika ngakhale akudutsa mmavuto osiyanasiyana.

A Mutharika womwe ali ndi achibale ambiri omwe Ali achipembedzo cha chisilamu afunira asilamu wonse mdziko muno pamene ali munyengo imeneyi ya Ramadani.

Follow and Subscribe Nyasa TV :

Sharing is caring!

Follow us in Twitter
Read previous post:
Chakwera ends two-week work from the North: Becomes first leader to work from Mzuzu State House that long

President Lazarus Chakwera has ended his 17-day tour of duty in the Northern Region, a development that has made him...

Close