Ana sukulu pa Soche Technical achita ziwonesero kamba ati akungodya nyemba basi

Kwavuta ku Soche Technical College ku Blantyre komwe ana a sukulu akutseka misewu kamba kokwiya kuti miyezi ikudusa koma akungolandira zakudya zomwe ndiwo zake ndi nyemba basi.

Wachiwiri wa Student Union Council pa sukulupo a Tiyanjane Chisowire wati ndiwodandaula chifuwa ma sabata akwana anayi tsopano chitsegulire sukuluyi koma ndiwo zimangokhala nyemba basi.

Mtsogoleri wa sukuluyi panopa akuyesesa kuti akambirane ndi ana asukuluwa ndipo chigulu cha a Polisi chafika kale kuzathandizira kubweresa bata.

Follow and Subscribe Nyasa TV :
Follow us in Twitter