Boma latsimikiza za chitetezo chokhazikika kwa achinyamata omwe akugwila ntchito dziko la Israel

Nduna ya zofalitsa nkhani yemwenso ndi m’neneri wa boma a Moses Kunkuyu wati kutsegula ofesi ya ukazembe m’dziko la Israel kuthandiza kuthana ndi mavuto omwe achinyamata akhathe kukumana nawo pomwe akugwila ntchito m’dzikoli.

A Kunkuyu ayakhula izi pa msokhano wa olemba nkhani ku Lilongwe pomwe mwa zina amatambasula za ulendo wawo wa ku Israel pamodzi ndi ndinu zina.

Tembo: Atetedzedwa

Iwo anati mgwilizano omwe mayiko awili-wa asayinilana uthandiza kuti achinyamata ambili athe kupita kukagwila ntchito za kuminda dziko la Israel mosavuta ndipo iye wati boma liyesetsa kugwila ntchito-yi mwa ukadaulo pofuna kukwanilitsa zomwe tsogoleli wa dziko lino Dr. Lazarus Chakwera adakhazikitsa pa ntchito-yi.

A Kunkuyu anaonjezelanso ponena kuti ndi khumbo la boma kuti achinyamata-wa adzitsata malamulo onse akagwilidwe ka ntchito-yi m’dziko la Israel molingana ndi momwe mgwilizano wawo ulili pofuna kusatsekeleza mwayi kwa achinyamata ena.

Kunkuyu wadzudzula m’chitidwe wa achinyamata ena omwe akumathawa malo awo ongwila ntchito ndikumapita malo ena ndipo wachenjeza achinyamata onse omwe akufuna kupita m’dzikoli kuti akhale olimbikila ndikuvala zilimbe pakuti ntchito yomwe ili ku Israel sikufuna munthu wa ulesi.

M’mawu ake nduna yoona za ubale wa dziko lino ndi maiko ena a Nancy Tembo anatsimikizila a Malawi komanso achinyamata m’dziko lino kuti dziko la Israel lili ndi kuthekela kolemba anthu ntchito za ukadaulo osiyanasiyana kuphatikizapo zomangamanga, zokopa alendo mwa zina ndikuti zikungofunika kuti achinyamata omwe akupita pakadali pano akakhale odalilila kuti mwayi wa magawo ena uthenso kutseguka.

Follow and Subscribe Nyasa TV :

Sharing is caring!

Follow us in Twitter
Read previous post:
FUM shakes Admarc to start buying farm produce to protect smallholder farmers

The Farmers Union of Malawi (FUM) has implored the Agricultural Development and Marketing Corporation (ADMARC) to start buying farm produce...

Close