Chakwera akhululukira akaidi 35
Mtsogoleri wa dziko lino a Lazarus Chakwera akhululukira akaidi 35 ngati mbali imodzi ya chisangalalo choti dziko lino lakwanisa zaka 60 zodzilamulira kuchoka m’manja mwa atsamunda.

Malingana ndi kalata yomwe watulutsa unduna wa za m’dziko ndipo wasainira ndi mlembi wamkulu a Steve Kayuni, a Chakwera agwiritsa ntchito mphamvu zomwe malamulo aakulu a dziko lino amamupatsa pa gawo 89 (2) komanso gawo 111 la malamulo oyendetsera ndende za dziko lino.
Akaidi omwe akhululukidwawa ndi omwe akwaniritsa ndondomeko zonse zoyenera kukhululukidwa komanso kusintha ndi kuonetsa khalidwe labwino pamene amagwira chilango chawo.
Kalatayi yatinso a Chakwera wachepetsa zilango za anthu ena ndi miyezi 9 ngati njira yofuna kuchepetsa kuthinana kwa anthu mu ndende za dziko lino.
Chiwerengelochi ndi chochepa poyerekeza ndi anthu 2 298 omwe anakhululukidwa nyengo yomweyi chaka chatha.