Chakwera apempha apolisi kuti akhale osunga mwambo

Mtsogoleri wadziko lino a LazarusChakwera yemwenso ndi wamkulu kunthambi ya a polisi, wapempha apolisi mdziko muno kuti akhale anthu osunga mwambo.

Mukulankhula kwawo ku mwambo otsanzikana ndi ophunzira ku sukulu zanthambiyi, ku Blantyre, a Chakwera adati zimakhala zomvetsa chisoni kuona a Polisi kukhalanso oyamba kumphwanya malamulo. A Chakwera adati a Polisi ndi anthu ofunika kwambiri pankhani yosunga malamulo adziko lino.

 

Iwo adati a Polisi amagwira ntchito yopambana pankhani yoteteza ose omwe aphwanyilidwa ma ufulu awo.

 

“Kufunika kwa a polisi mudziko ndiye nkosayamba. Inuyo ndi amene mumatithandiza kusunga malamulo. Ndiinu amene mumatithan diza kupeza chilungamo wina akatiphwanyira ufulu, Ndiinu amene mumatiteteza kwa anthu ofuna kutizunza kapena kutichitira nkhanza. Ndiinu amene mwatithandiza kuthana ndi mchitidwe wa u Satana ofuna kupha abale athu achialubino. Ndiinu amene mwavuta ndi ma breathalyzer mmisewumu pofuna kuthana ndi chibwana cha anthu oyendetsa magalimoto ali chile dzelere. Ndiiunu amene mumawateteza a Malawi akamachita zionetsero malingana ndi ufulu wawo, ” Adatero a Chakwera.

 

A Chakwera adatsindika kuti bomalake lidzipereka kukhwimitsa chitetezo mdzikomuno komanso kutukula miyoyo ya ogwira ntchito zachitetezo.

 

Chakwera wati pamene amatenga utsogoleri wadzikolino, m’dzikomuno munali apolisi 13,500 okha ndipo kwa dzaka zisanu zokha, boma lake lasula apolisi pafupi fupi 6,000 kufikitsa chiwerengero cha apolisi pa 19,570 ndipo akufunitsitsa kufikitsa chiwerengero cha wapolisi m’modzi pa anthu 500 kuti chitetezo chikhale chokwanira monga mwa malamulo.

 

Iye adati  ndi odzipereka  kuthandiza apolisi kukhala moyo wabwino monga nyumba zabwino komanso ndi zipangizo zowathandiza pa ntchito yawo komanso malipiro abwino.

 

Pamwambo omwe umachitika lero, apolisi okwana 1, 367 ndi omwe amaliza maphunziro awo.  Mwa amenewa, apolisi oposa 500 ndi atsikana.

Follow and Subscribe Nyasa TV :

Sharing is caring!

Follow us in Twitter
Read previous post:
LUANAR stresses the need to intensify agroecology approach for food security and economic growth

The Lilongwe University of Agriculture and Natural Resources (LUANAR) through the Malawi Agro-Ecology Hub has stressed the need for the...

Close