Chakwera ayamikila Bungwe la Red Cross kamba ka ntchito zabwino zomwe bungweli lakhala likupanga

Mtsogoleri wadziko lino Dr Lazarus Chakwera lero wakumana ndi mlembi wamkulu wa bungwe la International Federation of Red Cross (IFRC) kuno ku Malawi a Jagannath Chapagain yemwe wangosankhidwa kumene.

Mmawu ake a Chakwera ayamikira bungwe la International Federation of Red Cross chifukwa cha thandizo lomwe bungweli limapereka kudziko la Malawi.

A Chakwera anathokoza bungweli maka pathandizo lomwe linapereka pomwe dziko lino limakumana ndi mavuto ogwa mwadzidzi.

“Ukamagwira ntchito ndi a Red Cross, umamva kuti uli ndi bwenzi lopezeka kaya masana kaya usiku. Red Cross ndi chiyambi cha chiyembekezo kwa a Malawi makamaka nthawi ya mavuto ogwa mwadzidzi,” anatero a President Chakwera.

Polankhulapo, a Chapagain anathokoza a Chakwera powalola kuti akumane nawo.
Iwo anati bungwe lawo lipitirira kuthandiza dziko la Malawi.

Chaka chatha dzino lino lidakumana ndi Namondwe oopsa yemwe adakokola mbewu komanso zoweto zochuluka kwambiri .

Koma Bungwe la Red Cross lidali patsogolo kugwira ntchito yopulumutsa a Malawi.

Follow and Subscribe Nyasa TV :

Sharing is caring!

Follow us in Twitter
Read previous post:
Abida Mia hails Chakwera for naming road after husband

Minister of Water and Sanitation Abida Mia almost choked with excitement on Saturday afternoon as he thanked President Dr Lazarus...

Close