Chakwera watsindika zakufunika kwa luso la makono ngati njira imodzi yotukulira maphunziro
Mtsogoleri wa dziko lino Dr Lazarus Chakwera watsimikizira nzika za dziko lino kuti boma lake lakangalika pa ntchito yotuluka luso la makono ngati njira imodzi yotukulira maphunziro mdziko muno.
Achakwera adati ndi cholinga chawo kuona ana akugwiritsa ntchito makina a computer komanso ma lamya akulu akulu a tabuleti.
Polankhula pa msonkhano wa chitukuko omwe anachititsa m’boma Dedza a Chakwera adati cholinga cha izi ndikutukura komaso kumangaso Malawi watsopano.
Mtsogoleri wa masomphenyayu wati anthu mdziko muno adekhe chifukwa zinthu mdziko muno zibwelera mchimake ndipo aliyese pompano awona zipatso zake.
Dr Lazarus chakwera walangiza makolo mdziko muno kuti awonetsetse kuti akutumiza ana ku school osati kuwakakamiza ku mabanja pofuna kupeza zosowa zawo.
Pam’sonkhanopo a Chakwera anapempha makolo muti asabereke ana omwe sangathe kuwasamala.
Mtsogoleri wa dziko lino wachenjezanso nzika za dziko lino kuti apewe kunyoza komaso kupangira nkhaza anthu achikulilewa ponena kuti ndi mfiti.
Dr Lazarus chakwera anamaliza ndikunena kuti iye ngati mtsogoleri wa aliyese mdziko muno apitiliza kugwira ntchito zotumikira wina aliyese ndipo awonetsetsa kuti zitukuko zikugawawidwa mosakondera mbali komaso mtundu uliwonse chifukwa Malawi ndi mmodzi.