Chipani cha PP chati chiziwa za tsogolo lake mu Tonse Alliance kumapeto kwa chaka chino

Chipani cha People’s (PP) chati tsogolo pa mgwirizano wake ndi zipani zina pansi pa mgwirizano wa Tonse udziwika kumapeto a chaka chino pamene chipanichi chikhale chikuchititsa msonkhano wake waukulu pa 7 September mu mzinda wa Lilongwe.

Kalaile Banda

Wofalitsa nkhani za chipanichi a Ackson Kalaile Banda wati nthumwi za chipanichi zokwana 400 ndi zomwe zidzakambirane ndi kugwirizana za tsogolo la mgwirizanowu, mwa nkhani zina zomwe zikakambidwe ku msonkhanowu.

A Kalaile atsindika kuti chipanichi ndi cholimba ndipo chikupitirira kukonza ntchito zake m’madera osiyanasiyana mdziko muno.

Woyankhulapo pa nkhani za ndale a George Chaima ati zipani zandale zikuyenera kugwiritsa bwino ntchito mkumano waukulu ponena kuti umapereka mwayi kwa zipani kuti zikonze zofooka zake.

A Chaima atsindika kuti pakadali pano palibe chipani chimene chiri ndi kuthekera kodzaima ndikupambana pa chokha potengera malamulo a 50+1 percent zimene zikufunika kuti zipani zikonze ntchito zake ndikudzachita mgwirizano zisankho za chaka cha mawa zisanachitike.

Chipani cha PP ndi chimodzi mwa zipani zimene zidachita mgwirizano wa Tonse pa chisankho chachibwereza cha mtsogoleri wa dziko cha chaka cha 2020.

 

Follow and Subscribe Nyasa TV :

Sharing is caring!

Follow us in Twitter
Read previous post:
New Kid on the block: Sina Makossah releases ‘Good Vibes’ tune

There is a new kid on block on the scene and he appears to have come with a bang and...

Close