DPP ikuyenera kudekha pochotsa Nankhumwa pa mpando wa mtsogoleri otsutsa ku parliament, atero katswiri

M’modzi mwa oyankhula pankhani zosiyanasiyana, Wonderful Mkhutche walangiza chipani chotsutsa boma cha DPP kuti chidekhe pa chiganizo chake chochotsa Kondwani Nankhumwa ngati mtsogoleri wa aphungu otsutsa boma ku nyumba ya malamulo.

Sabata latha, chipanichi chinasankha George Chaponda ngati mtsogoleri watsopano wambali yotsutsa munyumbayi kulowa m’malo mwa Nankhumwa.

 

Koma pakadali pano, bwalo lamilandu laletsa kuchotsedwa kwa Nankhumwa pa udindowu kamba koti Nankhumwa anakadandaula pankhaniyi.

 

Malingana ndi Mkhutche chipanichi chikuyenera osaikoka nkhaniyi pakadali pano m’malo mwake chilemekeze chiletso cha bwalo lamilanduchi.

 

Katswiriyu akuona kuti mwayi ulipo kutsogoloku ozasintha mtsogoleri pa udindowu mopanda vuto lililonse.

 

Ndipo lero kunyumba ya malamulo, George Chaponda anabwenzedwa kukhala nawo pa mkumano wa adindo oyendetsa zokambilana munyumbayi kamba ka chiletso chomwe Nankhumwa anakatenga ku bwalo la milandu

 

Follow and Subscribe Nyasa TV :

Sharing is caring!

Follow us in Twitter
Read previous post:
Airtel gets 10-year renewed license, touts its over K50bn contribution to MACRA

Airtel Malawi PLC managing director Charles Kamoto, says the company has paid over MK59.4 billion to MACRA for levies, fees...

Close