Kazako pays tribute to Malawi music icon Wambali: Declares hope to an end to Covid-19 in a poem

Minister of Information and Communication Technologies, Gospel Kazako, has paid a rare tribute to music legend, Mtebeti Wambali Mkandawire, by sprucing up a poem in honour of the internationally recognised artist.

Mkandawire died of Covid-19 at the Kamuzu Central Hospital on Sunday morning.

Mte Wambali

His death has shocked both ordinary Malawians and high ranking officials in the Tonse Alliance government.

In his poem, which already gone viral on the social media, Kazako described the death of Mtebeti, as he was popularly known, as very painful.

Below is the poem:

 • Tamenyetsa manja kumtengo/ Dzinja lobereka kuwawa/ Tsozi lodontha lopanda chisusu chochita zotheka/
 •  Ndi mmasayamu muli chinyontho/ Chomwe chikulemba mtsizo/ Mtsizo yakulemberera umo mkudutsa misozi/ Nkubadwitsa kusisima kosalekeza.*
 •  Komabe tikudziwa/ Sikale pomwe tisiye kusisima.
 •  Tikudziwa/ Sikale pomwe njere zamoyo wa mweee! Tizifesenso/ Kuti tikolore zomwe tinazolowera kuchita.
 •  Sikale pomwe tidzasonkhane pansi pa kuwala kwa mwezi/ Kumayimba nyimbo zochokera ku nthano zotikumbutsa za chipsinjo chomwe chinali pakati pathu/ Chipsinjo chomwe chinatitseketsa pakamwa/ Ndi kutiwumiriza kusamba zipangizo zathu zodyera/ Ndi kulozera ndi sopo wa thovu nthawi zonse / Dera lokhala zala, manja ndi zikhadabo.
 •  Sikale pomwe tonse tidzatonthole/ Kutonthola kogwirana manja, kukumbatirana ndi kuchitira nkhomaliro limodzi. Kumavina!
 •  Izizi zitha! Izizi zigonja! Izizi tipambana! Izizi zikhala mbiri chabe. Mbiri yomayikamba, kusamvetsetseka!
 •  Koma izizi! Zitha!
 •  Tiyende mchigwa ndi miyendo ya mphamvu/ Tidziuyang’ana mthunzi ndi maso a chiyembekezo/ Tidziunong’oneza kuti sitili tokha/ Sitili tokha/ Sitili tokha!
 •  Uja wolenga dzuwa/ Maso ake ali pa ife/ Mmanja mwake / Atakwapatira chigonjetso.
 • Yendani bwino Wambali/ Yendani bwino Mtebeti / Pitani bwino Mtebeti / Kauseni Mtebeti!
 • Poti za kulimbana nako kwabwino/ Ndi komwe kukutipuputira misozi / Misozi yodzadza mzikope zamaso athu.
 • Muli ndi malo kumeneko/ Komwe inu mkupita! Kauseni Mtebeti!
 • Koma izizi, zitha!*

Follow and Subscribe Nyasa TV :

Sharing is caring!

Follow us in Twitter
5 Comments
newest
oldest most voted
Inline Feedbacks
View all comments
John chidongo
1 year ago

Ndi nthumadzi iyi inu a Kazako ndi boma lanu anthu akulirani mwaphetsa anthu miyanda miyanda ndi kulubwa lubwa kwanu. Ku Mozambique kumweko anthu sakufa ngati kuno kwanthu. Pano Chilimayo wangoti ziii ngati walowa chigoba cha fulu. Musatinyase ife. Kuyang’anira muvi watilowa mmaso tsopano kusowa chochita. Likakhala dyera la ndalama tsopano mukudya mwathumadzi mwaphetsa ndi muphetsa anthu ambiri. Nthendayi ili mu phweya tikupumiranawo mwari anthu anse afawa samavala mask, samasamba mmanja. Mwapanga mbiri a boma la alayasi padziko yolilitsa aMalawife. Pano ndiye mwati kukangalika. Tikulirani a Malawi mpaka kale kale. Paja mumamati nthanda yayikulu ndi dpp. Mulungu wakutsutsani. Mulibe mtendere mitima… Read more »

Phuma kachilima.
1 year ago

Inu a Nonse Alliance, please continue hugging each other as ordered by your own Arafat Hamdan chilima. There is no covid-19 in Malawi.

Bizarre
1 year ago

Covid-19: The Movie: survival of the slimmest.

Watondeka Chakwera
Watondeka Chakwera
1 year ago

Don’t waste our time Mr. Kazakh, you have forgotten that your Tonge Alliance told Malawian that there is no COVID-19.

Cairo
Cairo
1 year ago

Mbuzi zimenezi have contributed a lot to the spread of the virus in Malawi. You cheated Malawians that there is no covid in Malawi, this is what it means now, people are mourning and inu muli busy kulemba ndakatulo, nonsense. Misozi yaolira ili pamitu panu.

Read previous post:
Abida Mia set to mask up thousands of Malawians against Covid-19 for free after donating cow to ‘Feed the frontline’ initiative

Grieving deputy minister Abida Mia is set to make hundreds of thousands masks to be donated to Malawians across the...

Close